Wafika Nyau King ku South Bend, koma JB ati tisasilire: akukayimba ku Bwandilo ya ku Amereka

Advertisement
Limbani Kalilani

Oyimba wa kale wa chamba cha hip hop Jolly Bro (JB) akupitirizabe kuthira makala a Malawi a ku South Bend ku Amereka. Pano waonjezera mkwiyo kwa mkulu wa dambwe Tay Grin. Ati kumene akukayimba kumeneko ndi pa ma tharaveni basi. Bola Namadingo amayimba mma sitediyamu ku Lusaka.

Mu uthenga wina umene wapereka kudzera pa Facebook anthu ena ataonetsa kukwiya ndi mnyozo umene anamukhuthulira Lulu, JB waonjezera moto ndipo wati anthu ambiri amene akubwekera kuti oyimba athu ali kunja ndi osadziwa chabe.

“Akuti akubwera akukayimba pa Cool Runningz, pamalo pake sikuti ndi posilirikatu. Sikuti anthuwa akukayimba ku Hollywood. Akukayimba pa ma resitiranti, ndi pa Bwandilo penipeni,” anatero JB monyogodola.

Iye wati oyimba a ku Malawi akapita kunja sikuti amadziwika ndi komwe. Amangosangalatsa ma tchona basi amene ambiri mwa iwo ati akukhalira kudya mang’ina ndi nsima kumeneko.

“Kuti mufunse munthu aliyense kuti Lulu ukumudziwa kapena Tay Grin, palibe angawadziwe ndi komwe kuno. Ndi anthu osadziwika kwenikweni. Akamayenda palibe ali nawo ntchito,” anatero JB.

Iye anatafuliranso a Malawi okhala ku SouthBend amene akuoneka kuti wawapsera mtima atamuyenda chinyamata pa nkhani ya show ya pa 29 April pano.

“Ku South Bend anthu ake ndi a chimidzi. Ndi anthu osadziwa ndalama. Amangokuwalirani ku Malawi ngati ali ndi ndalama koma kuno ndi a mphawi angokhalira ngongole,” anatero JB.

Iye anafotokoza kuti matchona ena ali kumeneko angokhalira kuseta nkhalamba kuti apeze kangachepe.

“Ena mpaka amagona komko kusamala anthu, akamaliza azikuwalirani a Malawi,” JB anatero.

Pa 29 akuti kukhala dansi ya mkokemkoke ku Bwandilo kapena kuti Stereo ya ku Amereka kumene Lulu ndi Tay Grin avinitse a Malawi a ku SouthBend.

Advertisement