Yemwe anapeka nyimbo zachikatolika Pankalasiyo Phiri wamwalira

Advertisement

Mkulu yemwe analembanawo nyimbo za buku lachikatolika otchedwa Pankalasiyo Pondani Phiko Phiri wamwalira m’mawa wa lero lachiwiri.

A Phiri amwalira ku Nyumba kwawo ku Mua ndipo amachokera M’boma la Dedza.

A Phiri ndi m’modzi mwa anthu omwe analembanawo buku la nyimbo zachikotolika ndipo imodzi mwa nyimbo zi ndi “Chuma Chathuchi”, nyimbo yomwe imayimbidwa panthawi yopereka zambale pa mwambo wachipembedzo chachikatolika .

A Phiri amwalira patadutsa masiku ochepa chabe pamene akuluakulu komanso ogwira ntchito ku wayilesi ya Kanema ya Luntha anapita kukawaona komanso kucheza nawo powakumbukira ntchito zomwe anapanga.

A Phiri adabadwa mchaka cha 1940 ndipo amachokera m’mudzi mwa Kankhande kwa mfumu yaikulu Kachindamoto m’boma lomweli la Dedza.

Thupi lawo liyikidwa m’manda ku mudzi kwawo mawa lachitatu pa 19 April 2023.

Follow us on Twitter:

Advertisement