Timu yampira wa miyendo ya azibambo imakondeledwa — watero Tabitha


Mtsogoleri wa timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino yomwe osewera ake ali azimayi, Tabitha Chawinga, wadandaula ndikusowa chithandizo choyendesera timuyi.

Chawinga wauza nyuzipepala ya Nation kuti dziko lino lilibe chidwi chotukula mpira wa azimayi komanso wadandaula ndikukondeledwa kwa timu ya azibambo.

Tabitha wanena izi posatira kulengezedwa koti timu ya azimayi itha osatenga nawo gawo pa masewero ofuna kuzigulira malo mu mpikisano wa Paris Olympics 2024, kamba kakusowa kwa makobiri.

“Anzathu a ku Zambia amathandizidwa mokwanira ndi boma lawo pamene kwathu kuno timangodalira bungwe loyendesa mpira wa miyendo la FAM.

“Kumbali ya chithandizo, makampani samathandiza mpira wa azimayi. Tikuyenera tizilandira chithandizo chofanana ndi timu ya azibambo,” watero katswiriyu.

Osewera kutsogoloyu wanenanso kuti zikhala zovuta kuti timu ya azimayi izachite bwino ngati chithandizo chizisowa chonchi.

Izi zikugwirizana ndizomwe ena mwa otsata masewera ampira wamiyendo akhala akudandaula. Anthu amati timu ya Flames imathandizidwa kwambiri ngakhale simachita bwino, pamene ya azimayi imaonesa tsogolo lofika patali.

Follow us on Twitter:

Discover more from Malawi 24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading