Misonkho ya a Malawi: Ma alawasi abowoka ku UNGA

Advertisement

Pomwe a Malawi ochuluka akudandaula za mavuto adzaoneni pankhani ya zachuma, anthu omwe aperekeza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ku nsonkhano wamayiko (UNGA), akhala akupuma moyo wina akabwera kumudzi kuno, pomwe malipoti akusonyeza kuti anthuwa apatsidwa ma alawasi anyo!

Malingana ndi nyuzipepala ya Malawi News yomwe yatulutsidwa lero pa 17 September, 2022, ofeso ya mtsogoleri wa dziko ndi nduna (OPC), inavomeleza kuti anthu omwe apelekeza a Chakwera ku UNGA akalandire malawasi kawiri kuposa poyamba.

Nyuzipepalayi yati poyamba munthu amene wapelekeza mtsogoleri wadziko ku ulendo ngati uwu, amapatsidwa $280 (yomwe ikupitilira K280, 000) patsiku limodzi ngati alawasi koma pano anthuwa alandira ndalamayi kawiri.

Izi zikutanthauza kuti munthu wamba yemwe wapita nawo kunsonkhanowu, azilandira pafupifupi K592,000 patsiku limodzi zomwe zikutanthauza kuti kwa anthu omwe akhale kunsonkhanowu kwa masiku 15, akamabwera kumudzi kuno akhala ali ndi pafupifupi K9 miliyoni.

Mbali inayi, nyuzipepala ya Malawi News yati, nduna zomwe zapelekeza mtsogoleri wadziko paulendo ngati uwu poyamba zimapatsidwa K450,000 patsiku limodzi ngati alawasi ndipo mmene zatelemu zikutanthauza kuti nduna imodzi ilandira ndalama yopitilira K900,000 patsiku limodzi.

Malawi News yalembaso kuti pamasiku onse omwe anthuwa akhale ali ku nsonkhanoku, nduna imodzi ipatsidwa ndalama zosachepera K25.7 miliyoni pomwe alembi amaunduna osiyanasiyana komaso akuluakulu ena amaunduna agawana K131.3 miliyoni ngati ma alawasi awo.

Kupatula ndalama za ma alawasizi, boma likuyeneraso kupeleka ndalama za mayendedwe ndipo kuonkhetsera pa anthu 37 omwe apita nawo ku nsonkhanowu, boma likuyenera kupeleka ndalama yosachepela K174 miliyoni, kulipira ndege.

Mtsogoleri wa dziko lino wanyamuka kupita ku nsonkhanowu pa 12 September ndipo malingana ndi unduna owona zaubale ndi maiko akunja, mtsogoleri wa dzikoyu afika kuno kumudzi pa 2 October.

Pakadali pano, anthu ochuluka akudzudzula ofesi ya mtsogoleri wa dziko ndi nduna kaamba kovomeleza kuti anthuwa alandire ma alawasi ochuluka chonchi pomwe a Malawi ambiri akulira kaamba kakusayenda bwino kwa chuma.

Anthu ena mmasamba amchezo ati izi ndi ndalama zomwe zikanatha kugwira ntchito zina zachitukuko ndicholinga chofuna kufewetsa umoyo wa anthu mdziko muno komaso ena ati izi zikutanthauza kuti a Chakwera akulephera kukwanilitsa malonjezo awo.

Posachedwa, a Chakwera anaika ndondomeko zosiyanasiyana zofuna kuonetsetsa kuti ndalama za boma sizikusakazidwa makamaka pano pomwe chuma chadziko lino chikuyenda motsimphina.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.