Mkaidi awulura momwe analowetsera mafoni awiri m’matumbo mwake

Advertisement

Mkaidi yemwe lachitatu anadabwitsa anthu kaamba kopezeka ndi mafoni awiri m’matumbo mwake kundende ya Zomba, wati analowetsa mafoniwa kudzera ku malo ochitila chimbudzi ndipo waulura kuti akaidi ambiri ali ndi anthu omwe amawapititsira mafoniwa kundendeko.

Mkaidiyu yemwe dzina lake ndi Frank Siposi, lachitatu pa 11 May, 2022, m’mimba mwake munapezeka mafoni awiri othobwanya koma anyuwani, amtundu wa Itel omwe akuti anawalowetsa kudzera kumalo kwake kopangira chimbudzi.

Malingana ndi mneneri wa ndende mdziko muno, a Chimwemwe Shaba nkhaniyi inadziwika kaamba koti akuluakulu ena a ndende ya Zomba anadabwa momwe amayendela komanso maonekedwe ake.

A Shawa anati akuluakuluwa anatengela mkaidiyi kuchipinda kwina ndipo atampanga chipikisheni anadabwa kuona tizingwe kumalo ake ochitila chimbudzi, ndipo atamupanikiza ndi ndimafuso, mkaidiyu amaulura kuti walowetsa foni m’mimba mwake.

Koma malingana ndi kilipi (clip) yomwe tsamba lino lapeza yomwe a Siposi anajambulidwa pomwe amafusidwa mafuso ndi apolisi, iwo anachita kutumidwa ndi mmodzi mwa anthu owayang’anira yemwe akutchulidwa kuti Kachiganda.

Mkaidiyu anati a Kachiganda ndi omwe anawauza iwo kuti alowetse mafoniwa m’mimba kudzera ku malo ochitira chimbudzi pogwiritsa ntchito mafuta ophikira kuti asave kuwawa kwambiri polowetsapo.

Mukilipiyi, a Siposi akuvekaso akuuza apolisiwa kuti pa mafoniwa awiri wa, imodzi imayenera kukapelekedwa kwa mkaidi mzake dzina lake Yasin Kasonthi, pamene inayo anati amayenera kuigulitsa kundende komweko pa mtengo wa K40,000.

“Kachiganda anatitenga akaidi folo kupita kunyumba kwawo komwe anatipatsa mafoni awiri kenaka tinapita kudimba kwawo kukathilira ndipo titamaliza anandiuza kuti ndiike mafoniwa m’mimba kuti tizibwelera mkati, kenaka ine ndinaika koma mtafika mkati muno kuti ndiwatulutse sizikutheka.

“Foni inayi amati ndimpatse Yasin Kasonthi amubweretsera akazake, inayi amati ndigulitse K40,000 komano simnawapatse chifukwa choti alimmimbamu akukanika kuchoka. A Kachiganda anandiuza kuti ndiwaike mafoniwa mujumbo kenaka ndipake mafuta mkulowetsera kochitira chimbudziku ndipo amati zimakatuluka pokachita chimbudzi,” anatelo nkaidiyu.

A Siposi anauzaso apolisiwa kuti iwo ndikoyamba kupanga izi koma awulura kuti pali anthu ena omwe amalandira mafoni kuchokera kwa amzawo komaso achibale awo ndipo ati mafoniwa amalowa nawo kundendeko.

“Kunjaku ena amawabweretsera ndi azimayi awo ena azimzawo, monga White ali ndi mkazi wake amene amamubweretsera ma foni komaso pali wina wa pa 1 koma ndamuiwala dzina lake, nayeso,” anaonjezera choncho Siposi.

Advertisement