Gomani awuza Chakwera kuti achotse ntchito omunamiza

Advertisement

Mfumu yaikulu ya angoni a kwa Maseko am’boma la Ntcheu, Inkosi ya Makosi Gomani yachisanu, yawuza mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera kuti achotse mmaudindo onse omwe akumamunamiza komaso omwe sakugwira bwino ntchito yawo.

Inkosi ya Makosi Gomani yachisanuyi imayankhula izi lolemba ku Ntcheu pa msonkhano wa chitukuko omwe mtsogoleri wa dziko linoyu anachititsa atamaliza kuyendera mbeu m’bomali.

Mfumuyi inati a Chakwera komanso wachiwiri wake a Saulos Chilima akuyenera kuzindikira kuti anasankhidwa ndi anthu ochuluka osati ochepa omwe amuzungulira ndipo yati ndikwabwino kuti adindowa azichita zokomera aMalawi onse.

Apa Inkosi Gomani anauza a Chakwera m’maso muli gwaa kuti ayambe kuchotsa ntchito anthu onse amene amamunamiza komanso onse amene akubweretsa chisokonezo pakagwiridwe ntchito kawo m’ma udindo aboma.

“Apulezidenti ndinali ndi pempho, panthawi imene mwabwera chonchi mkuona zinthu mmene zilili, anthu amene mukugwira nawo ntchito akamapezeka kuti wina wakunamizani kapena sakugwira ntchito moyenera, apulezidenti muziwachotsa paudindowo.

“Izi ndukamba chifukwa choti inuyo monga pulezidenti mulibe ngongole ndi wina aliyese, ngongole yomwe muli nayo mwina ndiya aMalawi onse ngati dziko osati munthu aliyese payekha payeka ndipo akamapezeka ena obweletsa kachisokonezo, ziwachotsani ndithu apulezidenti,” yatelo Inkosi Gomani.

Kuwonjezera apo, mfumuyi inawuzaso a Chakwera kuti ngakhale kuti dziko lino likukumana ndi mavuto kaamba ka nkhondo yapakati pa Russia komaso Ukraine, nkwabwino kuti mtsogoleriyu apeze njira zotulukira mmavutowa.

“Zikumveka kuti kwavuta ndi Ukraine, mkhondo ya Ukraine ndi Russia ikubweretsa chisokonezo. Inde zoona apulezidenti ndiyovetsa chisoni nkhondo imeneyi komano ifeyo monga a Malawi, titsogoleleni kuti eya indedi izozo mzovuta, koma panopano tikambe zoti Malawi tidutsamo bwanji munyengo yomwe tiliyi,” inaonjezera chonchi mfumuyi.

Pankhani yaulimi, Inkosi Gomani inati anthu aku Ntcheu chaka chino sakolora chakudya chikwanira, choncho akufuna kuti boma liwathandize komaso yati ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo ikuyeneleka kuinikidwaso bwino.

Iwo anapempha a Chakwera kuti chaka chino akamadzapeleka mbeu mundondomeko ya zipangizo zotsika mtengo, azayambe kaye afufuza kuti mbeu yoyenera dera limenero ndi iti osati kungopeleka dziko lonse mbeu zofanana.

Mfumuyi inapemphanso boma kuti lilimbikitse ulimi wa mthirira komanso kulima mbewu ndi ziweto za makono ndi zosiyanasiyana.

Advertisement