A Kalindo ayimitsa kaye zionetsero

Advertisement

M’modzi mwa anthu omwe akhala akutsogolera a Malawi ku ziwonetsero zomwe zakhala zikuchitika mdziko muno posachedwapa, a Bon Kalindo, alengeza kuti ayimitsa kaye ziwonetsero zonse zomwe anakonza kuti zichitike.

A Kalindo omwe amadziwika ndi dzina la Winiko, akhala akutsogolera ziwonetsero za “Malawi salibwino” zomwe amati cholinga chaka kunali kufuna kukakamiza boma la Tonse kuti litsitse mitengo ya zinthu zina komaso kuthetsa katangale.

Koma pamene a Malawi amayembekeza kuti awuzidweso masiku komaso malo omwe zionetsero zina zichitike, mkuluyu wabweza phazi lake ndipo walengeza kuti wayamba waima kaye kuchititsa zionetserozi.

A Kalindo omwe amayankhula pa msonkhano wa atolankhani Lachinayi mumzinda wa Lilongwe ati ganizo loyimitsa kaye zionetselozi labwera potsatira ngozi ya madzi osefukira yomwe yaoneka m ’madera ena mdziko muno.

Apa iwo ati akufuna kupeleka mpata kwa boma komaso mabungwe kuti akwanitse kuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi ya madzi osefukirawa kaamba ka namondwe wotchedwa ANA.

A Kalindo atiso aganiza zoimitsa kaye zionetserozi kaamba poti awona kuti boma la Tonse motsogozedwa ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, ayamba kuyesetsa kuchita zomwe iwo akhala akupempha kuti zichitike.

Iwo ati boma la Chakwera likuyesetsa kwambiri kuthana ndi mavuto womwe iwo akhala akupeleka mu ziwonetsero zam’mbuyomu ndipo ati kuimitsa zionetseloku ndikupeleka mpata kuti boma lipitilize kukonza zinthu mdziko muno.

“Sitingapitilire ndi zionetselo zomwe tinakoza kuti zikhale zikuchitika m’madera osiyanasiyana mdziko muno. Tapanga chiganizochi titaunikira bwino bwino zomwe zakhala zikuchitika mdziko muno pakatipa.

“Zambiri zomwe zachitika pakatipa zikusonyeza kuti boma lili ndichidwi chambiri tsopano pakuthana ndimavuto omwe anthu mdziko muno akukumana nawo ndipo zambiri mwaizo ndi zomwe ife takhala tikupempha kuti zichitike,” atero a Kalindo.

Mkuluyu anauza atolankhani omwe anapezeka pansonkhanowu kuti ndiosangalala kuti boma la Tonse linamva pempho lawo ndipo lakwanitsa kutsitsa mtengo wa ndalama umene magalimoto akumapeleka akamadutsa pa zipata za pa Chingeni komaso Kalinyeke.

Iwo atinso ndiokondwa kuti boma lakwanitsaso kusintha nduna mzake komaso kuchotsa pa udindo nduna yakale ya zamalo a Kezzie Msukwa omwe akuganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi nkhani za katangale.

Izi zikubwera pomwe a Bon Kalindo amangidwapo kangapo pofika lero kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana kuphatikizapo kulumikiza magetsi ku nyumba yawo ya ku Lilongwe mwachinyengo

 

Advertisement