Tithana ndi aliyese ochita m’bindikilo pa Chingeni, Kalinyeke – atero apolisi

Advertisement

Boma kudzera ku nthambi ya polisi, lakaniza a Malawi kukachita m’bindikilo pa Chingeni komaso Kalinyeke pomwe eni magalimoto akumapeleka ndalama akamadutsa ponena kuti kutero ndi kuphwanya malamulo adziko lino.

Izi ndimalingana ndichikalata chomwe nthambi ya polisi yatulutsa Lachisanu pa 21 January chomwe wasainira ndi ofalitsa nkhani wankulu wa polisi a James Kadadzera omwe awuza anthu kuti asatenge nawo gawo pa m’bindikilowo.

Mu mchikalatachi a Kadadzera ati gawo 237 la malamulo ozengera milandu m ’dziko muno silimalora anthu kuti achite chili chonse chomwe chikubweretsa chisokonezo pakayendedwe ka magalimoto pansewu uli onse.

Apa apolisi ati motsata malamulo akathana ndi aliyese amene akapezeke akuchita m’bindikilo omwe malingana ndi a Bon Kalindo omwe akutsogolera, ukuyenera kuyamba sabata yamawa Lachiwiri pa 25 January, 2022.

“Ife a Malawi Police Service (MPS) tikudziwa zoti mzika zina za dziko lino zikufuna kukachira m’bindikilo pa zipata zotolelera ndalama za Chingeni komaso Kalinyeke. Anthu akuyenera kudziwa kuti gawo 237 ya malamulo ozengera milandu imanena kuti ndimlandu kusokoneza anthu oyenda pansewu.

“Ndiyeno mwaichi, m’bindikilo omwe wakozedwawu ndimlandu ndithu, choncho ife apolisi motsatira malamulo athu othanilana ndi milandu tikathana ndi aliyese amene akapalamule mlandu umenewu,” atelo a polisi.

A Kalindo mogwirizana ndi bungwe la eni ma minibasi ayitanitsa m’bindikilowu ati pofuna kukakamiza boma kukoza zinthu zina pakatoleledwe ndalama pamalo otolelera ndalama Chingeni ku Ntcheu komaso Kalinyeke ku Dedza.

Poyankhula pa msonkhano wa atolonkhani posachedwapa, iwo ati akufuna kuti munthu yemwe walipira ndalama pa Chingeni asamakalipileso ndalama akafika pa Kalinyeke chimodzimodziso kwa yemwe walipira kale koyamba pa Kalinyeke.

Mkuluyu akuti akufunaso kuti anthu asamalipile ndalama ngati akubwelera ku ulendo wawo pasanathe maola 24, zomwe ati ndikubera anthu ponena kuti munthu akalipira koyamba akuyenera azalipileso pakadutsa maola 24 osati zomwe zikuchitika pano.

Pakadali pano a Bon Kalindo omwe anachititsa zionetselo Lachisanu ku Blantyre komwe kunali khwimbi la anthu, sanayankhulepo pachikalata chomwe nthambi ya apolisi yatulutsachi.

Advertisement