M’bindikiro ulipo pa Chingeni sabata ya mawa – Kalindo

Advertisement

Amene akutsogolera zionetsero zotsutsana ndikusayenda bwino kwa zinthu m’dziko muno a Bon Kalindo, ati ngati boma siliyankha pempho lawo pa nkhani ya katoleledwe ka ndalama pa malo otolera ndalama ku magalimoto a Chingeni komanso Kalinyeke, iwo sabata yamawa atseka malo onsewa.

A Kalindo omwe amayankhula pa msonkhano wa atolankhani Lachitatu ku Blantyre ati akufuna kuti boma likonze zinthu zina pa momwe likuyendetsela malo omwe magalimoto akumapeleka ndalama akamadutsa a Chingeni komaso Kalinyeke.

Iwo anauza atolonkhani kuti ngakhale kuti boma linatsitsa pang’ono mtengo odutsira  pamalowa, iwo sakusangalatsidwa ndizoti eni magalimoto azipeleka ndalama pamalo onse awiri.

Apa a Kalindo ati akufuna kuti eni magalimoto omwe akuchoka ku Blantyre kupita ku Lilongwe akapereka ndalama pa Chingeni asamakapelekeso ndalama pa Kalinyeke Chimodzimodziso kwa omwe akuchoka ku Lilongwe kupita ku Blantyre.

“Choyambilira tiwayamikile aboma kuti anatsitsa mtengo ngakhale kuti sanafike pa K500 pomwe ife timafuna. Komano izi zomati munthu azipeleka ndalama pa malo onse awiri sitikugwilizana nazo, uku ndikuwabera aMalawi dzuwa likuwala.

“Tikufuna kuti ngati munthu wapeleka ndalama pa Chingeni, akamakadutsa pa Kalinyeke asakapelekeso ndalama, akuyenera akangowonetsa lisiti kuti wapeleka kale ndalama ya tsiku limenelo osati zomwe zikuchitika pano zomapeleka ndalama kawiri pansewu umodzi,” atelo a Kalindo.

A Kalindo atiso ngati munthu akubwelera komwe anapita tsiku lomwelo pasanathe maola 24, sakuyeneraso kupeleka ndalama paliponse ndipo ati ngati boma silimva mapemphowa, sabata yamawa kuyambira Lachiwiri pa 25 January akatseka malo a Chingeni komaso Kalinyeke.

Kalindo

“Izi zomati ukamabwelera ku Lilongwe kuchokera ku Blantyre uzilipiraso ndalama pa malo onse awiri, ndikuwabera aMalawi. Ngati ukubwelera kuulendo wako pasanathe maola 24, sukuyeneraso kupeleka ndalama iliyonse.

“Nde izi tinayankhula kalekale koma boma silikumva ndipo ndi chifukwa chake tikuti m’bindikilo ulipo kuyambira pa 25 January pa Chingeni ndipo ngati tipeze ndalama zokwanira pa nthawiyi tikatsekaso malo a Kalinyeke,” anaonjezera a Kalindo.

Iwo ati magalimoto omwe akaloledwe kudutsa ndiokhawo onyamula odwala, onyamula maliro, a polisi komaso asilikali ndipo ati ngati magalimoto ena akafune kudutsa akawalora koma ati akaonetsetsa kuti akadutse ulele.

A Kalindo atsimikizaso kuti zionetselo zomwe zinalepheleka sabata yatha ku Blantyre zichitika sabata ino Lachisanu pa 21 January koma adzudzula apolisi pobalalitsa anthu omwe anasonkhana kuti achite zionetselozo.

Iwo ati zomwe anachita apolisi pomanga anthu ena, nzosaloledwa pamalamulo kaamba koti iwo anatsata njira zonse zoyenera poitanitsa ziwonetsero zimenezo ndipo apempha kuti izi zisachitikeso Lachisanu lino.

A Kalindo atsimikizaso kuti awuzidwa ndi apolisi kuti zionetselo za Lachisanu zikayambire pa Zubeda osatiso pa Midima ponena kuti panali chiopsezo choti malonda akanatha kusokonekera mu msika wa Limbe

Advertisement