Abusa a Chakwera musiye kumanga anthu a kum’mwera – Mutharika

Advertisement

Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika, omweso ndi mtsogoleri wa chipani cha DPP, wawuza mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera kuti asiye kuzunza anthu achigawo chakum’mwera ponena kuti iwo pokhala m’busa sakuyenera kumachita tsankho.

A Mutharika amayankhula izi Lamulungu pa 19 December pa bwalo la Njamba mumzinda wa Blantyre pomwe chipani cha DPP mogwirizana ndi chipani cha UDF chinachititsa msonkhano wandale komwe kunali khwimbi la anthu.

Malingana ndi mtsogoleri opumayu, zinthu zambiri sizikuyenda bwino mdziko muno ndipo anati ndizokhumudwitsa kuti a Chakwera sakuonetsa chidwi chofuna kuthana ndimavuto omwe anthu akukumana nawo.

A Mutharika anati ndizokhumudwitsa kuti a Chakwera ngakhale ali m’busa akupanga mchitidwe wa tsankho ponena kuti anthu ambiri omwe akulembedwa ntchito pano ndi achigawo chapakati komwe a Chakwera amachokera.

Iwo anatiso chopweteka kwambiri nchakuti a Chakwera akuchitira nkhaza anthu amchigawo chakummwera makamaka anthu antundu wachilomwe ndipo apempha mtsogoleri wadziko linoyu kuti asiye zimenezo.

“Abusa a Chakwera inu ndi munthu wa Mulungu, ndikupempha kuti musiye kuzunza anthu akummwera komaso musiye kuzunza anthu a mtundu wa chilomwe chifukwa palibe chimene analakwa nde musiye zimenezo ndikukupemphani kwambiri. Muyambe kuyendetsa dziko lino.

“Patha chaka ndi miyezi 6 koma palibe chimene chikuchitika, choncho pangani zoti muyambe kuyendetsa dziko lino bwino komaso muyambe kupanga zija munkawalonjeza a Malawi zija,” atelo a Mutharika

Iwo anawuzaso a Chakwera kuti asinthe komanso kuchepetse chiwerengero cha nduna zawo komaso owathandizira ponena kuti nduna zambirizi zikungoononga chuma chaboma koma sizikukwanitsa ntchito zawo.

A Mutharika anadzudzulaso boma la Tonse motsogozedwa ndi a Chakwera kaamba komanga anthu omwe akumachititsa zionetsero kuphatikizapo a Bon Kalindo komaso a Sylvester Namiwa a bungwe la CDEDI.

“Bon Kalindo anawamanga kaamba kochita zionetsero koma a Chakwera, a Chilima, Mtambo ndi Trapence anachita zionetsero koposera chaka, kuononga zinthu, kuvulaza anthu koma ine sindinawamange chifukwa munthu aliyese ali ndi ufulu oyenda mmisewu kudandaula. Musiye zimenezo,” anawonjezera a Mutharika.

Masapota a DPP ndi UDF ku msonkhanowo

Iwo anadzudzulaso mipingo, magulu ndi mabungwe osiyanasiyana kaamba kongokhala chete osayankhulapo pomwe zinthu sizikuyenda bwino mdziko muno ndipo anapempha mafumu komaso mipingo ya mchigawo chapakati kuti iwaitanitse ndikulangiza a Chakwera.

Ndipo m’mawu ake, mtsogoleri wa chipani cha UDF a Atupele Muluzi anati a Chakwera ndi munthu wabwino koma ati vuto lalikulu ndiloti sakuchita malonjezo omwe ankanena panthawi yakampeni.

“A Chakwera ndi munthu wabwino koma sanasunge malonjezo awo. Anthu akufuna zomwe ankauzidwa nthawi yakampeni. Anthu akufuna chakudya, mankhwala, ntchito 1 million komaso feteleza wa mtengo otsika kwa onse zomwe anati adzapanga akadzalowa m’boma,” watelo Muluzi.

A Muluzi omwe anapempha kupitilira kwa mgwirizano wa zipani za DPP komaso UDF, anatiso mavuto ambiri akubwera kaamba koti a Chakwera anangofikira kukhala mtsogoleri wa dziko pomwe sanakhalepo nduna ndipo ati sakudziwa kachitidwe kazinthu m’boma.

Ena mwa akuluakulu a DPP kuphatikizapo wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi mchigawo chakum’mwera a Kondwani Nankhumwa, msungichuma a Jappie Mhango komaso mlembi wamkulu a Grezelda Jefule sanapezeke pansonkhanowu

Advertisement