Ndikufuna kukumana ndi Chakwera – watero Winiko

Advertisement

Amene akutsogolera zionetsero zosagwirizana ndi kukwera kwa mitengo ya zinthu Bon ‘Winiko’ Kalindo wanenetsa kuti akufuna akumane ndi mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera.

Kalindo amene adalepherana kumvana ndi nduna zaboma pamkumano omwe anali nawo sabata lapitali, wati ndiokonzeka kukumana ndi mtsogoleri wa dziko lino kuti akambirane m’mene angasinthire zinthu.

Polankhula ndi nyumba zoulusa nkhani, Kalindo watsimikiza kuti sadagwirizane ndi mfundo za nduna za boma zomwe adakumana nazo. Choncho, madando awo akufuna akapereke okha kwa a Chakwera.

Katswiri wa zisudzo yu amenenso ali phungu wakale wa mu boma la mulanje adakumana ndi nduna zinayi zaboma.

Bon amene ali mtsogoleri wa kale wa achinyamata mu chipani cha UTM, adakumana ndi nduna yoona za chitetezo Richard Chimwendo Banda, nduna ya mgwirizano wa mdziko Timothy Mtambo, nduna yofalisa nkhani Gospel Kazako komanso nduna ya za Chilungamo Titus Mvalo.

A Kalindo anenetsanso kuti boma likapanda kuchitapo kanthu pa ma pempho amene adapereka kudzela mu zionesero zomwe adatsogolera mu mizinda ikuluikulu itatu ya dziko lino, iwowo apitiriza kutsogolera zionetsero mu ma boma osiyanasiyana.

Advertisement

One Comment

  1. Anthu sakukhululupilililani ngati mupite kukakumana ndi Chakwera chikhulupililo cha wanthu chithera pomwepo

Comments are closed.