Ngati sali pa mseu, ali m’mwamba – Nankhumwa adzudzula Chakwera

Advertisement

Mtsogoleri wa zipani zotsutsa mu nyumba ya malamulo, Bambo Kondwani Nankhumwa, adzudzula mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kamba kolephela dziko la Malawi.

Polankhula mu nyumba ya malamulo, a Nankhumwa anati boma la a Chakwera lalephela. Mwa zina, iwo anatchulapo kukwela mitengo kwa zinthu ngati umboni wa kulephela kwa a Chakwera.

A Nankhumwa anaonjezelapo kudzudzula a Chakwera kamba kokonda ma ulendo, mmalo molabadila ofesi yawo.

“Amangokhalila kuyenda, ngati sali pa mseu ndiye kuti ali mmwamba pa ulendo,” anatelo a Nankhumwa.

A Nankhumwa ananena izi pamene mkumano wa nyumba ya malamulo ukupita kumapeto.

Iwo ananyodola a Chakwera kuti ulendo wa ku Kanani umene analonjeza a Malawi wakanika pamene chuma cha dziko lino chikunkelankela kuyipa.

Iwo anaonjezelanso kudzudzula a Chakwera kamba kolephela kusankha nduna zina kuti zitenge malo a ma unduna omwe eni wake anachotsedwa kapena kumwalila.

Advertisement