Rambo Onesimus avula chi Khristu

Advertisement
Onesimus show

Chaka chino ndiye kwatuluka nyimbo, koma Solomon ndiye yamangilira. Iyi ndi nyimbo yokuti imachita kumveka ndi mphanvu. Komanso uthenga wake ndiokoma zedi. Paliponse imatiimilira

Nyimbo iyi ndiye imakoma paja amati: “Chikhritsu mwachisiya kuti mwasanduka Van Damme/ Pena ngati Rambo mwalowa jungle jungle“. Nyimbo imakoma apa chifukwa pamatsindika kut ndeu kuti ichitike ndiye kuti chikhristu munthu umakhala wachivula kale.

Ndiye poti fan anachita zobhowa ku phwando lazamaimbidwe dzulo, Mmwini nyimbo anangoona kuti alowe Jungle apange zosiya chikhristu kuti aonese anthu kut za Rambo ndi Van Damme ankaimba zija amazisata. Anangovumbulusa theche apa pakana nkhani yafika kuma area.

Kumapeto kwake tivomeleze kuti anthu okonda kapena oonera za luso ndiobhowa. Ali ndi mfundo zodabwisa, amatha kusambwaza artist, ndipo amayankhula ngati kulibe mawa. Zina oimba akamva pakana kudabwa kuti ndiwe wemwe amene akumunena umu. Koma kumapeto kwake munthu waluso suyenera kuonesa kuti uli ndi mphuno ngati Rambo kapena kuonesa kuti malemba a Solomon okuti umukonde basi ulibe nawo ntchito. Koma muzonse tivomeleze Solomon ndichinyimbo chabwino zedi. Ndipo tiivina uku tilulandira mateche.

*Views in this opinion piece are those of the author

Advertisement