Mulomowu! A Chilima, a Mtambo ndi JB akukumbutsidwa chipongwe chawo pa Covid-19 chaka chatha

Advertisement

Ukayenda, siya phazi poti ukasiya mlomo umakutsatila. Mawu awa aphelezela pamene a Malawi akumbutsa akulu akulu a Tonse pa mawu a mnyozo ndi kudelela anakamba zokhudza mliri wa Covid-19 mu nthawi ya kampeni chaka chatha.

Ma kanema amene anthu anasungila ndiwo akunka akukumbutsa akuluakuluwa kuti mau m’samatha.

Mu kanema mmodzi, wachiwili kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima akumveka akuchenjeza boma la nthawi imeneyo la a Mutharika kuti lisiye kunena bodza pa nkhani ya Covid-19 ati poti maiko oyendeledwa ndi Covid-19 akumaonetsa maliro.

“Mu maiko amene muli Covid, akumaonetsa odwalawo ndi omwalila pa kanema, kuno ali kuti?” akudabwa choncho a Chilima amene amazitamandila kuti ndi ‘mfana oganiza bho’.

A Chilima anauzaponso owatsatila kuti azikumbatilana ndi anthu a Kongeresi ati kuti sangapatsane matenda. A Malawi ena akumbutsila za nkhaniyi ndipo ena akumbutsila lonjezo limene iwo ananena loti nyumba zina za boma zizasandutsidwa zipatala zosungako anthu odwala Covid iwo akalowa m’boma.

“Chitani munanena zija, sandutsani chipatala nyumba za boma,” anakumbutsa motelo a Malawi ena.

Nayo nduna yoona zophunzitsa anthu ndi kubweletsa umodzi ku Malawi a Timothy Mtambo agwidwa nkhwiko ndi mawu omwe.

Iwo analemba chaka chatha pa tsamba lawo la Facebook kuti boma la pa nthawiyo linali kuchita bodza ndi nambala za anthu odwala Covid-19.

“Mukuonjezela nambalazo achibale, mukukokomeza matenda wa. Si zoona,” analemba choncho a Mtambo.

Mtsogoleri wa kale wa dziko lino amene naye analowa nawo mu Mgwilizano wa Tonse, a Joyce Banda, nawo atsatilidwa ndi mlomo wawo umene anausiya ku Nkhatabay.

Kanema wina akuonetsa Mayi Banda akukana kuti ku Malawi kulibe matenda a Covid-19, iwo anati boma lingofuna chabe kupempha ndalama ku maiko a kunja.

Advertisement