Mpungwepungwe ku malo ogulitsira fetereza otchipa ku Zomba

Anthu ochokela m’midzi ya mfumu yaikulu Mulumbe komanso Chikowi ku Zomba ati ku malo omwe fetereza otsika mtengo akugulitsidwa m’bomalo kukumakhala mpungwepungwe chifukwa cha kusapezeka kwa apolisi.

Fetereza otsika ntengoyu wayamba kugulitsidwa dzulo m’madera ena m’bomalo, koma apolisi m’malo ogulitsira fetelezayu, monga pa Thondwe, apolisi sakumapezekapo.

Idzi zinadzetsa mpungwempungwe pomwe anthu amalimbirana kuti agule.

M’modzi mwa anthuwa yemwe anakana kuzitchula zina, anati kusapezeka kwa a chitetezo pa malowo kukuchititsa kuti kagulitsidwe ka feteleza kasakhale ka ndondomeko.

“Kusapezeka kwa achitetezo pa malo ano kukuchititsa kuti kagulitsidwe ka feteleza otsika ntengoyi kasakhale kosatsatira ndondomeko.

“Anthu tayima kwa nthawi yaitali komano mzere sukusuntha, anthu ena sanayime pamzere ndipo ndi omwe akupeza mwayi ogula fetelezayi,” adatero bamboyo.

Bambowo anawonjezelapo kuti kusapezeka kwa achitetezo pamalopo kutha kupangitsa kuti anthu ena aziyambitsa zipolowe pamalopo.

Chifukwa cha mpungwempungwe omwe unali pamalopo tidakanika kulamnkhulana ndi omwe akugulitsa fetelezayo.

Ku mbali yawo, a Joseph Sauka, yemwe ali mneneri wa apolisi mu chigawo cha ku kuzambwe (east) anati kusapezeka kwa apolisi m’malowo kunangowona kuchitika komano apolisiwo monga achitetezo amayenera kuti azipezeka malowo.

Pakuona kwawo a Sauka anati vuto litha kukhala loti omwe akugulitsa fetelezawo sanapite kukakamba ndi apolisi kuti akhala akuyamba kugulitsa feteleza kuti apolisiwo apange dongosolo lopita mkumakhakhazikitsa bata mmalo omwe akugulitsilamo feteleza otsika Mtengowo.

Ngakhale izo zili choncho iwo anati afufuza chomwe chinapangitsa kuti mmalowa musapezeke apolisi, komanso atumizamo apolisi oti azikakhazikitsa bata ndi mtendere mmalowa komanso m’malo onse akugulitsila feteleza otsika mtengoyi.

Advertisement