Tipita kukhothi ngati sitiyankhidwa – atelo amayi

Advertisement

Amayi omwe amachita zionetsero lachisanu zosakondwa ndi kusaikidwa kwa azimayi ambiri m’maudindo aboma, ati ngati mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera sawayankha madandaulo awo, atengera nkhaniyi ku bwalo lamilandu.

Wanena izi ndi Maggie Kathewera Banda yemwe anatsogolera azimayi omwe anachita zionetserozi lachisanu mu mzinda wa Blantyre.

Kathewera

A Kathewera Banda ati zomwe anachita a Chakwera posankha azimayi ochepa m’maudindo osiyanasiyana ndizochititsa manyazi kwambiri kaamba koti mtsogoleri wa dziko linoyu akudziwa bwino zomwe malamulo amanena pankhani yosankha maudindo.

Apa iwo anati malamulo adziko lino amanena kuti sizoyenera kuti maudindo ambiri azitengedwa ndi azibambo okhaokha ndipo anati iwo sakuwapempha a Chakwera kuti ayike azimayi ambiri mmaudindo koma akufuna zomwe zinanenedwa m’malamulo zichitike.

Iwo anati akudabwa kuti a Chakwera apangiranji izi pomwe nthawi yakampeni analonjeza kuti akazawina zisankho azaika azimayi ambiri mmaudindo.

“Uthenga waukulu omwe Ife tikunena ndi oti malamulo atsatidwe. Anthu awa asanalowe m’boma anatilonjeza kuti adzaonetsetsa kuti akuchita zinthu motsatira malamulo adziko lino nde lamulo lina ndi ilili lokhudza kuika azimayi mmaudindo lomwe tikufuna alitsatire.

“Nde Ife tikuti ngati iwowa angasankhe kusamvera zomwe malamulo akunena, nafeso tipita ku khothi monga momwe anachitira iwowo kuti akhale pomwe alipo ndipo tikukhulupilira kuti khothi likatithandiza chifukwa izi sitikukamba zam’mutu mwathu koma tikukamba zomwe zinalembedwa mmalamulo,” anatelo Kathewera Banda.

Mwantu wagalu a Kathewera Banda anakanitsitsa zomwe anthu akuyankhula zokuti mabungwewa atumidwa ndi chipani chotsutsa cha DPP kuti achite zionetserozi ndipo anatsindika kuti izi achita mwakufuna kwawo kuti malamulo atsatidwe ndipo palibe wawatuma.

Iwo anatiso sizikutanthauza kuti iwowo potsogolera zionetserozi ndekuti akufuna udindo koma anati pali azimayi ambiri omwe alindikuthekera koti atha kugwira bwino ntchito zomwe zikupatsidwa kwa azibambo okhaokha.

Iwo anati ndizosamveka kuti a Chakwera apemphe kuti apatsidwe nthawi yoti ayike azimayi mmaudindo kaamba koti nkhani yokhudza malamulo munthu amakakamizidwa kuchita nthawi yomwe zomwe malamulowo akunena kaya akufuna kapena ayi.

Izi zikudza kutsatira mndandanda wa anthu omwe a Chakwera akhala akutulutsa kuwasankha mmaudindo osiyanasiyana a m’boma omwe ukusonyeza kuti azimai ambiri sanaikidwe mmipandomu

Advertisement