Thyolo yakana bwanamkubwa Matchaya

Ganizo la boma kudzera ku unduna owona za maboma ang’ono ndi chitukuko cha kumidzi loti a Medson Matchaya apite ku Thyolo ngati bwanamkubwa wa bomali liunikilidwaso kamba kakuti makhansala komaso mafumu awakana a Matchaya.

Izi zaululika dzulo pa 3 August 2020 pa mkumano omwe akuluakulu amene adaimilila mlembi wamkulu wa undunawu adakumana ndi makhansala komanso mafumu.Poyakhulapo, a Alufeyo Banda omwe adaimila mlembi wamkulu adati cholinga cha mkumanowo kudali kuzatsimikizila madandaulo a athuwo pamaso ndi pamaso kutsatila kalata zomwe makhansalawo adalemba.

“Tilipano kuti timve ndi pakamwa panu ngatidi kalatazi mudalemba ndi inu chifukwa kalata zina zilibe ma siginechala. Kotero aliyese amasuke osaopayi ndipo zonse zomwe tikambilane pano tikawauza omwe atituma,” adatero Banda.

Mkatikati mwazokambilana, makhansala komaso mafumu adanenetsetsa kuti Matchaya sakumufuna kamba ka khalidwe lache.

“Mwanena kale kuti ngati unduna mutapita kukafufuza kwa anthu aku Nkhotakota mwapezadi kuti khalidwe la Matchaya silabwino kwa athu ake ogwila nawo ntchito. Komaso mwanena kuti ndizoonadi kuti mpaka pano miyezi khumi (10) yadusa ogwira ntchito pa khonsolo ya Nkhotakota osalandila malipiliro. Kutengera zimenezi, ifeso tikuti Matchaya kuno ayi,” adatero m’mozi wa makhansala.

Khansala wina adati: “Komaso taonani munthu sadayambe kugwira ntchito nafe, akutenga makhansala mwa mseli kupanga mkumano mkuwapasa ndalama. Uwu ndi upo afuna kugwilisa ntchito njira ya “divide and rule’ cholinga tigawanikane.  sitichita kupanga kampeni. zoti Matchaya abwere kuno ife takana.”

Nawoso mafumu adakana zoti a Matchaya akhale bwanamkubwa ku Thyolo.”Mbiri yoipa yatsogola kale pomwe muthuyo sanafike ichi ndi chizindikilo choti muthuyi akuyenera uphungu (discipline) osati kutumizidwaso kwina ayi. Kumeneko kuli ngati kusamusa vuto kupititsa kwina,” mfumu ina idatero.

Pakadali pano akulu akulu aku undunawu ati payenera kusankhidwa ogwirizira mpando wa ubwanamkubwa pomwe madandowa akhale akukaunikilidwaso.

Advertisement