Titseke maso tipemphele – Chakwera alengeza za kusala kudya kwa masiku atatu

Pamene mliri wa korona wayamba kufala mopanda mantha m’dziko muno, mtsogoleri wa dziko lino amenenso ndi m’busa Lazarus Chakwera wapempha kuti a Malawi asale kudya.

Mu chikalata chomwe chatulutsidwa ndi nduna yofalitsa nkhani komanso mneneri wa boma a Gospel Kazako, a Chakwera ati a Malawi athandizane nawo kusala kudya kwa masiku atatu.

“Tipemphelele onse omwe akhudzidwa komanso tiyika mmanja mwa Chauta onse amene sanakhudzidwe kudzanso anthu a chipatala,” watelo Chakwera kudzela mwa a Kazako.

Kusala kudya uku ati kuyambika lachinayi ndipo kudzafika pa mponda chimela lamulungu pamene anthu azapemphele kuthokoza Mulungu.

Malinga ndi uthenga ochokela ku boma, ati anthu azayamike Mulungu mnyumba mwawo kudzanso mu ma tchalitchi pa zinthu zomwe Yehova wachitila Malawi.

Advertisement