Ikatha Namazani, muwaona Atcheya pa kampeni – watelo Atupele

Ati akubwela kuzathandizila kampeni Atcheya Bakili Muluzi.

Atupele Muluzi wati mtsogoleri opuma amenenso ndi Bambo ake, a Bakili Muluzi, achita nawo kampeni yoti chipani cha DPP chipambane.

Atupele amene wakhala akuchita misonkhano yoimaima analengeza izi ku Zomba pa ulendo wake opita ku Mangochi.

“Andipatsila moni Atcheya, komanso ati ndikuuzeni kuti ikangotha nyengo yosala kudya iyi, abwela azachite nawo msonkhano,” anatelo Atupele uku omutsatila akuyimba m’manja.

A Muluzi anali mu dziko la South Africa kuchipatala ndipo afika ku Malawi sabata latha.

Chipani cha DPP chapanga Mgwilizano ndi chipani cha UDF chomwe anayambitsa ndi Bakili Muluzi.

Advertisement