President wa dziko lino Peter Mutharika wauza mtundu wa aMalawi kuti matenda a Covid-19 omwe akumayamba chifukwa cha Coronavirus apezeka mwa anthu atatu Ku Lilongwe.
Izi zadziwika pamene anthuwo anaonesa zizindikiro zina zamatendawa ndipo atayedzedwa ndi achipatala, zatsimikizika kuti anthuwo akudwaladi matendawa.
Mukuyankhula kwake, President Peter Mutharika wati munthuyo ndi mai yemwe anapita ku dziko la India ndipo atabwelako anadzipatula yekha.
“Anthu onsewo anali nyumba imodzi ndipo wina ndi m’bale wa maiwo pamene wina ndi munthu wantchito wa mnyumbamo. Tikuyesa kufufuza onse omwe anakhudzana nawo kuti akayezedwe matendawa,” watero President Peter Mutharika.
Poonjezerapo, pulezidenti wapempha aMalawi kuti akhale akusata njira zomwe zinakhazikitsidwa kuti zizisatidwa pofuna kupewa matendawa.
Boma laikanso njira zina zomwe zikuthandiza kuti matendawa asafale monga kulesa anthu kukhala m’magulu komanso kukhala moyandikana.
Matenda a Covid-19 anayamba mu December mu chaka cha 2019 ku China ndipo apha anthu ambiri mmaiko osiyanasiyana.
Malawi ndi dziko limozi mwa maiko ochepa omwe matendawa anali asanafike.