Wafika mkutho wachinayi wa Covid


…mapemphelo, ma bala, atha kuletsedwanso

Ngati munakomedwa ndi msonkhano wa a ndale pachiwelu paja ndi kumayesa zipitilila, muganize kawili. Mliri wa Covid wamanga nthenje moti a boma akukumana kuti akhwimitse kachikena malamulo.

Malinga ndi akatswiri a zachipatala, nambala za anthu amene akupezeka ndi kachilombo ka corona zachuluka ndipo zingosonyeza kuti nyengo ina ya Covid yafika. Pa masiku anayi apitawa, dziko la Malawi lakhala likuona nambala zochuluka za anthu opezeka ndi corona moti anthu amene analengezedwa lachiwiri pa 14 December anadutsa ma handede awiri.

Izi zadzetsa nkhawa ndi mantha kamba kuti mliri wa Covid tsopano ati ukufala mosavuta.

Koma malinga ndi nduna ya za umoyo a Khumbidze Kandodo, bungwe limene linakhazikitsidwa kuyang’ana za nkhani ya Covid likhala likukumana ndipo alengeza ngati ndi kofunika kusintha njila zotsatila pofuna kupewa chigodola cha mliri wa Covid.

M’mbuyomu, mkumano wa bungweli unapangitsa kuti malo omwela mowa atsekedwe komanso achepetse chiwelengelo cha anthu olowa mu ma kachisi ndi malo ena amkumano monga ukwati. Koma pakali pano malamulo okhudza mkumano anawachotsa.

Koma chikonzelo chobwenzeletsa malamulowa sichinakondoweze a Malawi onse. Anthu ena akutsutsana ndi a boma ati kamba iwo akuchita zinthu mmene akufunila.