M’modzi wa mamembala a UTM a Jessie Kabwila anena kuti a Malawi sakufuna kuona nyekhwe koma akufuna chitukuko, chlungamo komanso kulamuliridwa and atsogoleri okonda dziko lino.
A Kabwila, omwe anakhalapo phungu wa nyumba ya malamulo oimilira anthu a ku Salima, amayankhula izi pa mwambo omwe zipani za UTM ndi Malawi Congress zikuyembekezeka kusayanirana za mgwirizano wawo ku Lilongwe.
Malingana ndi a Kabwila, zomwe akumanena mtsogleri wa dziko lino a Peter Mutharika zoti otsutsa awona nyekhwe si zomwe a Malawi akufuna.
“Nkhani siyoti a Malawi azilamuliridwa ndi anthu ochita kumatiophyeza kut eeh muona nyekhwe. Zoona zaka 55 (zodzilamulira tokha) ife a Malawi tione nyekhwe? Zoona?” anatero a Kabwila.
Iwo anaonjezera kunena kuti anthu mu dziko muno akufuna a Lazarus Chakwera ndi a Saulos Chilimna chifukwa amakonda dziko.
A Kabwila ananenaso kuti anthu akufuna zintchito, chakudya chokwanira, chitukuko ndi fetereza otchipa.
“Mgwirizanowu wabadwa chifukwa tikufuna Malawi apite patsogolo,” anatero a Kabwila.