Bungwe lomenyera ufulu wa anthu m’dziko muno lomweso akuluakulu ake ndi omwe akutsogolera zionetsero la HRDC lalengeza kuti zionetsero ziyambilaso pa 27 mwezi uno zomwe ati zichitikira mu zipata komaso mabwalo andege a dziko lino.
Bungwe la HRDC likumakonza zionetsero pofuna kuti wapampando wa MEC a Jane Ansa atule pansi udindo wawo.
Lero bungweli kudzera mwa wa chiwiri kwa wapampando wake a Gift Trapence alengeza kuti kuyambira pa 26 mpaka pa 30 mwezi uno kudzakhala m’bindikilo m’mabwalo andege komaso mzipata zonse zolowera ndikutulukira m’dziko lino.
A Trapence anati izi ndikaamba koti a Jane Ansah mpaka pano sanatulebe pansi udindo wawo ngakhale bungweli linakoza zionetsero zazikulu sabata yatha zomwe amayembekeza kuti ziwapangitsa mai Ansa kutula pansi udindowo.
Iwo anati akudziwa bwino zomwe malamulo amanena pachiganizo chawochi ndipo ati pakadali pano adziwitsa kale makampani onse andege komaso anthu ochita malonda m’malowa zachikozero chawochi.
“Kuchokera pa 26 August mpaka pa 30 titseka zipata zonse zadziko limo komaso m’mabwalo a ndege onse a dziko lino. A Malawi akudziwa bwino lomwe kuti titamaliza ma demo athu akulu, Mai Jane Ansah sanatule pansi udindo mpaka pano.
“Pano tabweraso kuwauza a Malawi onse omwe ndi eni ake dzikoli kuti tipiteso kunsewu kukapanga m’bindikiro mpaka mai Ansa atatula pansi udindo wawo,” anatero Gift Trapence.
Mkuluyu anapitilira ndikunena kuti ngati pakutha panthawi ya m’bindikilowo mai Ansa adzakhalebe asantule pansi udindo monga momwe akufunira, bungwe lawo lidzaitanitsaso zionetsero zazikulu zina pa 5 September.
Iwo anati nkhani yaikulu kwaiwo siyoti anawina zisankho ndindani koma vuto ndi m’mene a Jane Ansa anayendetsera chisankhochi ponena kuti panachitika zachinyengo zochuluka ndipo anati sakufuna kuti mkulu wa MEC yu apitilire kukhala pa mpando
Afiti awa ana obadwira mchimbudzi osapola pa mchombo.Mudzafa amphawi agalu,anyapapi,agulukunyinda,agan’ga komanso mphemvu