‘Zochedwa ku ntchito ife ayi’ – a Malawi auza Chakwera

Advertisement

Pofika kumapeto a mwezi wa May ngati a Malawi angasankhe a Lazarus Chakwera a Malawi Congress Party (MCP) kukhala mtsogoleri wa dziko lino ndiye kuti kuntchito kuzizapitidwa mma 8 mmawa.

Mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha MCP walonjeza kuti akangolowa m’boma ndiye kuti iwo asintha nthawi imene anthu ogwila ntchito m’boma amayambila ntchito.

Chakwera wanyula

Polankhula pa msonkhano omwe anachititsa pa bwalo la Njamba mu mzinda wa Blantyre, a Chakwera ananena kuti chipani cha MCP chikalowa m’boma ndiye kuti nthawi yoyambila ntchito isintha ati Kamba akufuna kuti anthu azizakwanitsa kukonzekeletsa ana awo kupita ku sukulu.

Ngakhale kuti anthu ambiri anaombela mmanja mfundoyo a Chakwera atayinena pa msonkhano, a Malawi ambiri pa malo a mchezo a Facebook atsutsana ndi ganizoli ati Kamba ndi lobwenzeletsa chitukuko mmbuyo.

Pothililapo ndemanga pa tsamba lina loulutsa mawu litalemba za nkhaniyi, a Michael Gondwe analemba kuti:

“Zofunika ku Malawi ndi kuonjezela maola ogwilila ntchito ndi kuchepetsa masiku a tchuthi.”

A Marumbo Golden ananenapo kuti a Chakwera akulimbikitsa ulesi ndi maganizo awo ochepetsa maola ogwilila ntchito.

Pamene a Jack Bow ananena kuti a Chakwera akunena izi Kamba koti sanagwilepo ntchito iyayi kupatula ubusa basi.

Anthu ena koma aikila kumbuyo mtosgoleriyu ponena kuti mu maiko ambiri otukuka anthu ake amayamba ntchito 08:30 ndipo sikuti zimawasaukitsa monga ena akunenela.

Advertisement

One Comment

  1. Nkhani sikuchedwa kupita kuntchito. Akuti 08: 30 ndi nthawi yoyambila ntchito. Koma chomwe ma Civil Servant akusowa ndi nthawi yoyambila ntchito? Tiuzeni kuti the lowest paid Civil Servant will pocket so much, osati zanthawizo.

Comments are closed.