Mpingo wa Satana auvomeleza tsopano

Advertisement

Mpingo umene umazitcha okha kuti ndi mpingo wa Satana ndipo umazitcha kuti ndi oyamba pa dziko lonse lino kubwela poyela ndi kumamasuka kuti umapembedza Satana tsopano auvomeleza ngati mpingo oti usamapeleke msonkho.

Malinga ndi malipoti a nyumba zoulutsila nkhani za maiko a kunja monga Bloomberg ndi Mirror yak u Mangalande, Khoti lina ku Amereka lalamula kuti mpingo wa satana tsopano ukuyenela kumavomeledzedwa ngati chipembedzo.

Malamulo amene amatsogolera zipembedzo monga chiKhristu ndi chiSilamu akuti akhale malamulo omwewo otsogolera mpingo wa Satana. Mwa zina akuti anthu onse opeleka zinthu zawo monga chuma ku mpingowu azitengedwa ngati kuti akhoma msonkho.

Pamene mipingo ya ku Malawi kuno sipeleka misonkho ndiye kuti mpingowu utabwela ku Malawi kuno nawo suziloledwa kupeleka misonkho.

Mpingo wa Satana umene umapezeka ku Amerika iwo umanena kuti sukhulupilila za milungu ndipo iwo umapeleka mphamvu kwa munthu yoti azitha kuukila zinthu zimene sakugwilizana nawo, amene ndi makhalidwe anapatsidwa kwa Satana mu Baibulo.

Mpingowu umatsutsanso zoti mipingo izilowelelapo pa nkhani zandale.

Ngakhale iwo uli mpingo wa Satana sukhulupilila kuti Satana alikodi.

Mmbuyomu mpingowu unaika chifanifani cha nyama yomwe anthu opemphela amaitcha mdyerekezi ati pofuna kuti aonetse kusakondwa kwawo ndi malamulo khumi a Mulungu amene analembedwa pa chipilala china mu dziko la Amereka.

Mpingowu wakhalanso ukutsutsana ndi zokuti mapemphero azichitika mu sukulu za Amereka.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.