Pamene dziko la Malawi chaka ndi chaka likupitilirabe kumakhala likukumana ndi vuto lakusowa kwa madzi m’madera a ku midzi komaso mu matauni, katswiri wina wati kuvutikaku ndikochita kufuna.
Anthu ambiri mdziko muno amakhala akulilira kuutsi chaka chilichonse kaamba kakuvuta kwa madzi omwe amakhala asakutuluka mu mmipopi komaso mmijigo m’madera ochuluka posatengera kuti ndi nyengo ya mvula kapena ayi.
Chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga mchakuti zaka zino mvula ikubwera mwa njomba kutsatila kusintha kwa nyengo komwe ndikaamba kakuononga za chilengedwe monga mitengo yomwe imathandiza kubweretsa mvula yochuluka.
Tikulankhula pano anthu ozungulira pa boma ku Ntcheu alowa mwezi wa chisanu ndi chitatu madzi asakutuluka m’mipopi ndipo m’madera ena omwe kumachitika ulimi wamthilira ukukhala ovutilako masiku ano kamba koti ma damu ochuluka amadzi akumaphwela nsanga.
Koma nanga tingatani kuti tithetse vutoli ngati dziko? Katswiri wina yemweso ndimkulu wa gulu loona zokolora madzi a mvula mdziko muno la Rainwater Harvesting Association of Malawi, a Macpherson Nthara ati kuthekera kothana ndivutoli kulipo.
A Nthara ati kukolora madzi a mvula ndinjira yokhayo yopezekeratu yothanirana ndi vuto la kusowa kwa madzi mu mdziko muno ndipo ati njirayi mmaiko ambiri akuikonda kwabasi kaamba koti ilibe chiopsezo chili chose ku miyoyo ya anthu.
Iwo anena kuti ndiodandaula chifukwa chakuti dziko lino likutaya madzi ochuluka mu mnyengo ya mvula pambuyo pake mkumadandaulaso za kusowa kwamadzi mmalo momachita kholora la madziwa.
“Kukolora madzi amvula ndikotheka mumdziko muno potengera kuchuluka kwa mvula yomwe dziko lino limalandira koma mutha kuona kuti madziwa sitimawasamala amangotayika basi. Vuto lakusowa kwa madzi ndilalikulu ndipo tilindimadera ambiri amwe anthu atha kumakolora madzi amvula mosavuta koma mwayiwu sukugwiritsidwa ntchito.” Wadandaula Nthara.
Mkuluyu anaonjezera kuti nthawi yakwana tsopano yoti anthu mdziko muno akuenera kugwilana manja pankhaniyi ndipo ati bungwe lawo palokha silingakwanitse pozindikila kuti mutu umodzi siuseza denga ndipo apemphaso boma kuti liike chidwi chake pa nkhaniyi.
“Bungwe la Rainwater Harvesting Association of Malawi palokha silingathe tikuenera a Malawi tigwilane manja kuti tithese vuto lakusowa kwa madzi ndiposo ndipempho langa kuti boma liike njira zoti lithandizire anthu mma midzi kupeza zipangizo zokololera madzi amvula,” watero Nthara.
Iwo anaonjezeraso ponena kuti anthu athaso kukolora madziwa pokumba ngalande kuti madzi ochoka mmisewu azidutsa ndikuwapatutsira mma damu mmalo awo ochitira ulimi.
Malingana ndi a Nthara, pakadali pano bungwe lawo likumanga malo okololera mvula m’boma la Kasungu komaso Lilongwe koma ati malowa ndiosakwanira kukolora madzi ambiri ndipo apempha boma kuti lilowelelepo.
Pophera mphongo pa nkhani yokolora madzi amvulayi, a Kondwani Magombo omwe ndi mtolankhani wa Malawi News Agency (MANA) omweso pano akugwira ntchito ngati olankhulira khonsolo ya boma la Mangochi ati dziko lino lili ndikuthekera kotuluka mu mvuto la kusowa kwamadzili.
Bambo Magombo ati iwo nthawi ina anakhala ndimwai opita mdziko la Israel komwe mvula imavutilako kuyelekeza ndikuno koma mudzikoli kusowa kwamadzi ndi nkhambakamwa poti mvulayo ikagwa anthu amakolora madzi ake.
“Ndinapitako Ku Israel ndipo chomwe ndinaphunzira ndichakuti dontho lililonse la mvula mdzikoli lomwe mvula ndiyosowa kwambiri amalitenga lofunika kwambiri. Izi ndizomweso tikuenera kuchita ndipo tili ndikuthekera konse,” atelo a Magombo.
Iwo ati kupatula kukolora madzi a mvula dziko lino lithaso kumagwilitsa ntchito madzi kuchokera mnyanja yathu ndipo vuto lamadzi akumwa komaso ochitira ulimi wamthilira lingakhale mbiri yamake dzana.
“Nyanja ya Galileya ndiyotalika makilomita makumi awiri ndi mphambu imodzi (21km) ndipo mulifupi ndi khumi ndi mphambu zitatu (13km) pamene yathuyi ndi yaikulu ka khumi koma ife timakanika kuigwirisa bwino ntchito kuyelekezera ndi azathuwa omwe amaigwiritsa ntchito bwino ndipo vuto lakusowa kwamadzi linatheratu mdzikoli,” anaonjezera mtolankhani wa zachilengedweyu.
Padakali pano boma lili kalilikiliki ndi ntchito yotenga madzi kuchokera mmu mnyanja yathu, m’boma la Salima ndipo akuwapititsa mma boma oyandikila kuphatikizapo Lilongwe koma malingana ndi akatswiriwa ndondomekoyi itha kufikira angakhale dziko lonse la Malawi ngati patakhala upangiri wabwino.
Kusintha kwa nyengo padziko lonse komaso kuchuluka kwa anthu ndiko kwapangitsaso kuti vuto lakusowa kwamadzi lichuluke ndipo kukolora madzi a mvula ngati kutatsatidwa bwino ithadi kukhala njira yothanilana ndi vutoli.