Avipwantha, avikuntha, avisosola, aviyendesa mwa reverse  vinyerere

Advertisement
Carlsberg Cup

Mwana akatsogola ndi chikwama, si ndiye kuti ulendo ndi wake iyayi. Afunseni a neba anuwo kuti za Masters akutipo chani. Ngati akwiye, ndi a nyerere amenewo. Asekeni.

Ataonetsa ngati tsiku ndi lawo ndipo chikho cha Carlsberg akutenga, Manoma lero alilila kuutsi atapumunthidwa ngati neba wawo ndi migwanya yaku Lilongwe.

Pa masewero amene anachitikila pa bwalo la za masewelo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre, nyerere zinayamba ndi ukali pomwetsa chigoli mpira utangoyamba. Anzawo asakudziwa chimene chikuchitika ndi komwe, Manoma anaonetsa chamuna ndi kuyamba kutsogola.

Kunali chimwemwe ku Lali Lubani pamene amayesa Manoma afika pa mpunga ndipo zigoli mwina khumi acmwetsa ndi zina zisanu oyimbila achita kuleletsa.

Komatu kupeleka chibakera choyamba sikupambana ndewu, ndipo Manoma anaona kulungama kwa Chichewachi lero pamene anyamata a Masters Security anayamba kuphopha nyerere ndi zibonga moti pamene masewero amafika pokapumila ndi kuti Manoma akuti ndi mwayi chabe kuti snakomoke ndi zibonga.

Mu chigawo chachiwiri ndimo Manoma anaona ululu wa chibonga. Atateteza ka chigoli kawo koyamba kaja, basi kutatsala mphindi zisanu zenizeni kuti mpira uthe, migwanya inakhoma chibonga pamutu pa nyerere kuti adzetse mantha ndi chikayiko ku Lali Lubani.

Anakakamila anyamata a Masters mpaka masewero anafika ku ma penatem kaphera choka ndipo uko ndi kumene Manoma anafelatu. Maliro awo osanyamula, kungoika pompo pa Kamuzu.

Advertisement