Maliseche athu ndi Peter Mutharika – Ben Phiri

1

Timva zinthu chaka chino. Tiona zinthu pofika nthawi yovota mu 2019. Ngati ena sayenda buno bwamuswe chibadwile ndiye ndi mwayi chabe.

Peter Mutharika

Ben Phiri: Maliseche athu ndinu

Mkulu oyang’anila za chisankho mu chipani cholamula cha DPP a Ben Phiri wayelekeza a Peter Mutharika ndi maliseche.

A Phiri amene ali ponda apa n’pondepo wa a Peter Mutharika anauza anthu ku Zomba komwe amakawamema zolembetsa mavoti kuti iwo azavotele a Peter Mutharika.

“Maliseche munthu umabisa ako,” anatelo a Phiri.

Iwo anaonjezelapo kuti anthu a chigawo cha kummwera maliseche awo ndi a Peter Mutharika ndipo anayenela kuti voti yawo azapatse a Mutharika basi.

A Phiri amene amaziti ndi obadwa mwatsopano komanso ndi M’busa adzudzulidwa ndi a Malawi ena kamba kopepuza mtsogoleri wa dziko ndi kugwilitsa chitsanzo chosayenela.

 

Share.

One Comment

%d bloggers like this: