Ambiri ali pambuyo pa Chilima, achina Obama ndi Kasaila kumeneko – watelo Ngalande

Advertisement
Peter Mutharika

Sizili bwinotu a President ndipo ena amene akumabwela pamaso panu ndi kumati ndi anu, musawamvele chifukwa usiku akumanka nakanyonyomala kwa wachiwiri wanu kukachongetsa.

A Lewis Ngalande amene ndi mkulu wa achinyamata muchipani cholamula cha DPP ati ngakhale gulu likuoneka ngati likukonda a Mutharika, pansi pa mtima anthuwa akufuna a Chilima.

Lewis Ngalande
Ngalande: Ambiri akufuna a Chilima.

Mu chikalata chimene atulutsa chopita kwa a Mutharika, a Ngalande auza a Mutharika kuti adzuke ndi kuyamba kukonza chipani tsopano.

A Ngalande ati zimene akuchita a Mutharika zongokhala ngati mu chipani chawo mulibe mavuto ndi zibwana chabe chifukwa kugawikana muchipani ichi kwafika patali.

Iwo aulula anthu ena amene nawo akuimila kumbuyo kwa a Chilima kuwafuna kuti nawo atenge chipani cha DPP pa ulendo wa 2019.

“Musayese ndi a Kaliati, a Ngumuya, a Kalindo ndi a Masangwi okha. Kuli gulu uku,” alemba choncho a Ngalande.

Mwa ena, iwo ati kuli a Peter Kumpalume, a Malison Ndau, a Aaron Sangala, a Grace Obama Chiumia ndinso a Francis Kasaila amene akufuna kuti a Chilima atenge boma.