Amangidwa kamba konyoza President pa Facebook

Advertisement
Mangochi

Anthu awiri amene amatsogolera anzawo pochitila mtudzu President ndi kumema anthu kuti achite zionetselo anjatwa.

MangochiIzi zachitika mu dziko la Tanzania limene Mtsogoleri wawo John Magufuli wayamba kuonetsa makhalidwe achilendo ofuna kupondeleza ufulu wa anthu.

Malinga ndi malipoti, abambo awiri amene amalemba zoti anthu apite ku mseu posaonetsa kukondwa ndi nkhanza za a Magufuli ndiwo amene anatoledwa ndi Apolisi.

Zipani zotsutsa ku Tanzania zikumema anthu kuti pa 26 April apite kumseu ndi kukaonetsa kukhumudwa ndi utsogoleri wa a Magufuli amene sakukhala bwino ndi anthu osagwilizana nawo.

Magufuli anachenjeza onse okonzekela zionetselo kuti athana nawo mopanda mantha.

Advertisement