Mzimayi wauka kwa akufa Ku Ntcheu

Advertisement
Mayi ouka kwakufa

Mantha othetsa mankhalu agwira anthu a m’mudzi wa Bula mfumu yaikulu Kwataine m’boma la Ntcheu mzimayi wina yemwe anamwalira kumapeto amwezi watha ataukaso kwaukufa lamulungu koma pathupi pa miyezi isanu ndi iwiri pomwe anali napo patachoka.

Apolisi auza tsamba lofalitsa nkhani la Malawi News Agency (MANA) kuti azindikira mzimayi ouka kwa akufayu ngati Linesi Jana yemwe anaikidwa m’manda pa 26 Julaye chaka chomwe chino.

Mayi ouka kwakufa
Jana (pachiwiri kuchokela kumanja) kucheza ndi achemwali ake (Pic by Grace Kapatuka)

Mchemwali wa Linesi, Mary Sambi anauza nyuzipepala ya MANA kuti yemwe waukayo anamwalira pa chipatala cha Ntcheu pa 25 mwezi watha pomwe amadandaula kuti mutu umamupweteka kwambiri.

“Iyeyu kwakanthawi wakhala akudandaula kuti umamupweteka kwambiri ndipo patsikuli atadandaulaso tinamutengera Ku chipatala chaboma cha Ntcheu komwe anagonekedwa.
“Usiku umenewo azibale ake tose sitinagone chifukwa m’bale wathuyu amalira kwambiri ndi nthendayo ndipo mmawa wake anatisiya,” watero Mary, mlongo wa Linesi.

Iyeyo watsimikza kuti mtsikana waukayo ndi mlongo wake ndipo watsindika kuti ndiyemweyo komaso palibe chomwe chasintha pa thupi la mtsikana ouka kwa akufayo.

Mary wanena kuti chomwe chakhala chinthu chachilendo pa m’bale wawoyo ndichakuti pathupi pa miyezi isanu ndi iwiri pomwe anali napo nthawi ya imfa yake alibe tsopano komaso akuti akumalankhulaso chi Yao chomwe sanayambe walankhulapo ndipo kale lose.

Potsilira mang’ombe, mchimwene wake wamtsikanayu, Alfred Banda, wati nkhaniyi siyachilendo kwenikweni kamba koti anthu mderali akhala akuwauza kuti amuona Linesi koma akamuitana akuti amathawa ndipo samamupezaso.

Banda watsimikizaso kuti mtsikanayo ndi m’bale wawo ndithu ndipo ati ali ndi chimwemwe kuti amuonaso ngakhale zili zinthu zodabwitsa.

Malipoti a pachipatala cha Ntcheu atsimikiza kuti Linesi anagonekedwa pachipatalachi pa 24 mwezi watha ndipo anamwalira tsiku lotsatira lake.