Mzimayi wauka kwa akufa Ku Ntcheu

Mayi ouka kwakufa

Mantha othetsa mankhalu agwira anthu a m’mudzi wa Bula mfumu yaikulu Kwataine m’boma la Ntcheu mzimayi wina yemwe anamwalira kumapeto amwezi watha ataukaso kwaukufa lamulungu koma pathupi pa miyezi isanu ndi iwiri pomwe anali napo patachoka.

Apolisi auza tsamba lofalitsa nkhani la Malawi News Agency (MANA) kuti azindikira mzimayi ouka kwa akufayu ngati Linesi Jana yemwe anaikidwa m’manda pa 26 Julaye chaka chomwe chino.

Mayi ouka kwakufa
Jana (pachiwiri kuchokela kumanja) kucheza ndi achemwali ake (Pic by Grace Kapatuka)

Mchemwali wa Linesi, Mary Sambi anauza nyuzipepala ya MANA kuti yemwe waukayo anamwalira pa chipatala cha Ntcheu pa 25 mwezi watha pomwe amadandaula kuti mutu umamupweteka kwambiri.

“Iyeyu kwakanthawi wakhala akudandaula kuti umamupweteka kwambiri ndipo patsikuli atadandaulaso tinamutengera Ku chipatala chaboma cha Ntcheu komwe anagonekedwa.
“Usiku umenewo azibale ake tose sitinagone chifukwa m’bale wathuyu amalira kwambiri ndi nthendayo ndipo mmawa wake anatisiya,” watero Mary, mlongo wa Linesi.

Iyeyo watsimikza kuti mtsikana waukayo ndi mlongo wake ndipo watsindika kuti ndiyemweyo komaso palibe chomwe chasintha pa thupi la mtsikana ouka kwa akufayo.

Mary wanena kuti chomwe chakhala chinthu chachilendo pa m’bale wawoyo ndichakuti pathupi pa miyezi isanu ndi iwiri pomwe anali napo nthawi ya imfa yake alibe tsopano komaso akuti akumalankhulaso chi Yao chomwe sanayambe walankhulapo ndipo kale lose.

Potsilira mang’ombe, mchimwene wake wamtsikanayu, Alfred Banda, wati nkhaniyi siyachilendo kwenikweni kamba koti anthu mderali akhala akuwauza kuti amuona Linesi koma akamuitana akuti amathawa ndipo samamupezaso.

Banda watsimikizaso kuti mtsikanayo ndi m’bale wawo ndithu ndipo ati ali ndi chimwemwe kuti amuonaso ngakhale zili zinthu zodabwitsa.

Malipoti a pachipatala cha Ntcheu atsimikiza kuti Linesi anagonekedwa pachipatalachi pa 24 mwezi watha ndipo anamwalira tsiku lotsatira lake.

Advertisement

292 Comments

 1. Izi sizoyamba kuchitika ku Ntcheu. vuto ndi mtundu wa ufiti uli kumeneko, amakonda kumumwaliritsa munthu ali kadali ndi moyo. Nkhani yofananiranapo ngat imeneyi inachitikapo mu zaka za ma 1980 mudzi mwa matale T/A Phambala ku ntcheu komeko.

 2. Kutha kwa dziko zambili zizachitika osamadela nkhawa mukswona ndi kumva zotelozo zidikilani mawu a mwana wa munthu omwe analembedwa mu bukhu lopatulika

 3. Mayiwa ajambulitse nawo za uzika nawoso nd mzka ya malawi chonde apatsen mpata nd mzka yathu wabadwila ku malawi kachikena

 4. Balibe aliyese yemwe angaxaigonjese imfa koma imfayo kugonjesa anthu dziko lose la pansi. Comwe cinaikidwa m’bokosi sanali iyeyo koma masenga cabe, iye anatengedwa ndi xiwanda xoyipa. Mulungu akalamula ndiye walamula sabwelelaso mbuyo. Ixi ndi zizindikilo zakuntha kwa dziko.

 5. Well, its strange and hard to believe, did anyone come forward with information that the grave where she was buried into is vacant? Did news reporters confirmed this before printing the news out? How about the police? Did the health department carry out any tests confirming this? If none of these was done, am aware to take this as true. It was just a witchcraft motivated incident , however if anyone insist , then come forward with reports and prove this incident true.

 6. Maroza awa maroza eni eni. anamukupa uyu wathawako chiyao waphunzira kwa anzake kumene amagwira ntchitoko olo ine ndikadzafa mokupidwa ndidzauka ndidzakathawako.akadzandikaka mira adzatha onse pamenepo

 7. Pano ali kut mayiyu?Ndipo akusungidwa ndi ndan pot mukut amfumu akana.Sayenela kukana koma asadapite kwa achibale ake boma kapena kut Apolice amusunge munthuyo ndikumupitisa kumapemphero.Ngati mukut ndi zamuwanthu,Ndiye kut muziwe kut Mulungu si James sadakondwele nayo umfa yake kamupempheleleni ndipo akhaleso pakati panu poti naye ndimunthu ngati inu.Tangoganiza ali m’bale wanu mungamukane ?Afotokoza chomwe chidamuchitikira ngati wabwelela kapena kuukaso ndi mphamvu ya mwini wake wa m’mwambamo.Ngati mwapemphela ndi mtima wanu ose,mphamvu nanu zose ndipo mwakhulupilila Mulungu azakhala bwino kufikila siku lomwe Mulungu adamukozera.Ndikhulupilira mwandivesa.

 8. Sindikukhulupila zimenezi kodi munthu ake ndiutiyo pakati pa azimayi 4 alipansiwa koma zoona zimenezi, komangati ndizoona ine ndikoyamba kumva chibadwileni pamoyowanga e,e koma zisamba or chain makamaka zikundimvuta kumvetsa koma mwati ndizoonadi zakhaniyi.

 9. kunena chilungamo munthuyu sanafe Ku mamidziku Ku ma chitika zosayenela Ku makhala kuwelengana munthuyu anagulitsidwa Ku manda sana pite ameneyu analipo koma ana mugulitsa ufiti Ku ntcheu kwambili or pokaika Ku manda sikuti anakaika munthu yu ayi kuti akafukule aka peza chinthu cha chabe chake anthu amagulitsana Ku mafamu basi azikalima Ku meneko ulele akakhala kuti mulungu sana fune amakhala sana fune wa bwela munthu anapanga chipongwe ndi wa chiyao kuti mui brauze bho bho nkhani ndiufiti una kula pa munthu yu anamulowelela pama tenda ake amutu sikuti ana mwalila munthu yu wawathawila Ku meneko munthu anapangayo ndekuti amamu sunga mnyumba poyembekezela business yawo yoipayo anango tuluka mo mnyumba wa muthawila

 10. I don’t believe this how can a dead person rise to live again ? And who helped her to remove the stone cause the story said she was barried? Witch craft is real

 11. chiyao akuyankhulacho its because amene anamugula ndimuyao so chiyao anaphuzirira kumeneko,,,,anthuwa guys sakhala kt adzuka kwaakufa bt anthu amene anawapha mmatsengawo amakhala kt apanga release pafukwa chakt mwina munthuyo amakana kugwira ntchito ndizina zotero,mwinaso amakhala kt munthuyo wathawa yekha

 12. Kodi anapita kumandako natsimikiza kuti mdzenje lomwe adamfotseralo mulibemo? Ndi Yesu yekha amene anagonjetsa imfa.

 13. Paja ndi kuntcheu tu no wonder anthu amatha kusanduka afisi ndikumayenda. Komanso akamati imfa yagonja samathandauza kuuka kwake kosangwidwa mmatsengaku ayi, izo ndi za matsenga mkana amuchotsa mimbayo, kuuka komwe titanzauke tikafa siuku ayi. Mufufuzen bwinobwino ndithu.

 14. inu atolankhani tamayesetsani kufunsa mafuso okwanira kuti tidzimvetsetsa nkhani mwati pathupi panachoka chipatala anamuyesa? Nanga omwalirayo munafunsa kuti chinamuchitikira ndi chani? apolice akuchitapo chani kuti mchitidwewu ngati ndizoona uthe? the use of the national lDs wil help to verify because of finger prints please expand your investigations!

 15. I feel like the woman is an impostor, there is no way one can learn a new language while dead & then speak it fluently after resurrection, I’ll believe this only when am dead as well

 16. Komatu a Daniel Nkhoma afunsa funso lomwe silikuyankhidwa ndi abale kapena a polisio: KODI KU MANDA KUMENE MUDAKAMUIKA WO MWALIRA KULI BWANJI?? NDIPO PA NDEMANGAPO PAKUMVEKA KUTI YEMWE ADAMWALIRAYO AKUYANKHA KUTI ADALI KWA MFUMU: NANGA MFUMUYO MWAIFUNSA MASUNGIDWE AMZIMAIYO KUTI ADALI OTANI?? KUTSOGOLA SIKUFIKA!!!

 17. Wabadwa Mwatsopano Ameneyo,tamulandira Adzadye Nawo Cash Gate Ya Joyce Banda Akubweletsayo.Mafilu Mutiuze Zambili Za Graveyard Koma Fazi Akuti Ibwelako Liti Kubwerako Nanga Ndikusabwera Ngati?

 18. aaaah aja opangidwa zamatsenga aja awa koma amat zikatelo mitu yawo siigwila amakhala amisala or akangosowa kachiwili samabwelelaso…zinachitikakoso ku L cty i remember..

 19. Komatu azimayi tikuwaonawa apawa ndi amudzi mwa m’mbulu T/A Maganga M’boma la Salima osati Ntcheu so how come?

 20. ndye waukira kwachabetu nanga mmene mavuto alili ku malawi kuno iye ndkumadzukraso kuno osakazuka ku america bwanj shaaa mistake

 21. Alipo yemwe walephera matsenga ake pamenepo.koma akumbukile mau a ambuye yesu kunena kuti,tawonani ndidza msanga mphoto yanga ndili nayo yakupatsa yense monga mwa ntchto zace. Palibe chinsinsi chimene sichidzavumbuluka.

 22. Yesu yekha ndiemwe adauka kwa akufa ,awa ndi aja amazembesedwa mmasenga anthu kukaika bokosi lokha munthuyo mkumakawagwilisa ntchito Ku zigayo ndie akabwerako muli wauka kwa akufa ndi Satanatu uyu akukugwira ntchito simasewera

  1. vuto ndilakuti simuwerenga baibulo. mumangomvera kwa azibusa basi.. mupitenso kwa abusa anuwo akakuuzeni nkhani ya elisa kuti atamwalira chinachitika ndichani. atinkenawo inu

 23. Koma Ndawona Ine Ukulu Wanu Mbuye Pitilizan Kuwonesa Ukulu Wanu Yehova alangen anthu amene amachtla zamasenga anzawo plz musawalekelele alandle2 chilango pansi pano

 24. Ndizodabwitsa Zimenezi Chifukwa pathupipo Padapitakuti Ndizofunika Kuti Mulungu Aweluze Mwachangu Dzikoli Kuti Oguila Tchito Zobisika Adzaululike .

  1. Osati siameneyu adamwalirayo? Nduona ngati uyuyo ndi wina koma mwina mutu adasokonekera. Mwanene kale kuti akulankhula chinenero china. Alibe pathupi ngati momwe adapitira malemuwo. Bwanji alole achipatala amupime bwino-bwino?

 25. GUYZ ZINA TIYENI TIZILANKHULA Potengela U munthu umene tili nawo Kudzuka kwa munthu omwalilayu zikugwilizana bwanji ndinkhani zachipani? Nthawi zina ngati tilibe comment ayi ndithu ndi bwino kungokkhala osalankhula kanthu sikutinso mungaluze chili chonse, koma zinazi zimangooneselatu kusazindikila chomwe mukunena coz zimakhala zopanda phindu, pamalilo sipopangila ndale ndipo ngati mukufuna kutchuka ayi ndithu pezeni zina zitchukila osati zimenezo, zikukhudzeni ndipo muziganizile muli inu m,bale wanu wamwarila nde adzuke ngati zachitikilamo ena azilankhula mbwelela ngati mukulankhula apazi mungamve bwanji?

 26. Chikudabwitsa ndi chot mimbayo yapita kut? Nanga chiyaochi zitheka bwanj kuyankhula poti anali ngoni?Zitha kukhala kut ndi chiwanda chatsanduka ngat malemuwo.musaiwale kut ziwanda zimatha kusanduka ngat munthu.

  1. Zoona brother ndiponso nkhope imeneyo kwaine ai yachilendo ikufanana ndi mwana wa cousin sister wanga kwa Tambala village T/A Malembo m’boma labalaka ikufanana ndende osasiyana sure ndi imweyo ndithu

 27. Sikoyamba ku dedza zinachitikapo ukoo amati kuchipala zaka zapitazo koma mpaka pano ali ndi moyo zimakhala kt pali athu amene apangapo zao mumatsenga amakhala muthu amubisa pena pake inu ndikumalira chathochi ambuye weluzan dziko athu adziwe za ukulu wan

Comments are closed.