Kubwezera nkhonya kwakanika, South Africa yapamanthanso Scorchers kachiwiri

Advertisement
Scorchers

Timu ya Malawi ya mpira wa miyendo ya atsikana lero yafanso kachiwiri 2-1 ndi timu ya South Africa mu masewelo a pa ubale omwe anachitikira pa bwalo la Lucas Moripe m’dziko la South Africa.

Chigawo choyamba chinatha chetechete ndipo chigawo chachiwiri chitayamba mphindi zochepa chabe Malawi inapata mwayi wa kona yomwe anasema Ireen Khumalo kukapeza mutu wa Vanessa Chikupila yemwe anasumbira mu golo kuti ikhale 1-0.

Banyana Banyana inabweranso nayo ndi kona pa m’phindi ya 74 ndikupata chigoli chofananitsira mphamvu kudzera mwa Hilda Magaia 1-1

Malawi imakanika kupatsilana, kuimitsa mpira komanso kuvutika kukhazikika pa mpira ndipo atsikana a South Africa anawona kuti ndi mwayi wawo tsopano kuti akhazikike.

Pa m’phindi 86, South Africa inapeza freekick Amogelang Motau yemwe amasewera m’dziko la Mexico, anamenya bomba la mphamvu kuchokera panja pa 18 yard moyandikira mzere odula Katikati la bwalo. Bombali linakangomulowa otchinga pagolo Mercy Sikelo yemwe anangoima atatanula manja m’mwamba mpira n’kudutsa pompo 2-1.

Mapeto a zonse oyimbira amaliza wenzulo kuti zatha mokomera atsikana a kumapeto kwa Africa wa omwe tsopano awamba Malawi kawiri motsatizana pomwe ma timuwa akukonzekera masewelo a mu mpikisano wa WAFCON mu miyezi itatu ikubwerayi.

Mphunzitsi wa Scorchers Lovemore Fazili anavomeleza kugonja pomwe wati iwo agonja ndi timu yabwino, Banyanyana Banyana ndipo wayamikira atsikana ake ponena kuti akakonza mofowokamo.

Mphunzitsi wa Banyana Banyana Desiree Ellis wati masewelo a lero timu yake yangosewera bwino m’chigawo chachiwiri ndipo wati sanagonje chifukwa atsikana ake samataya mtima mwachangu pa masewelo aliwonse.

Iye watinso pena timu imatha kusewera udyo koma imapambanabe basi.

Timu ya Scorchers yagonja kachiwiri pomwe masewelo oyamba omwe anachitira pa bwalo la University of Johannesburg ku Soweto imafanso 3-0.