Ndine okonzeka kunjatwa – atelo Mayi JB

Advertisement
Joyce Banda & Oswald Lutepo

Mtsogoleri opuma wa dziko lino Mayi Joyce Banda amene dzulo Apolisi aulula kuti aupeza unyolo wa msinkhu wawo ati iwo sakunjenjemela ndipo ndi okonzeka kuuvala unyolowo.

Joyce Banda
Mayi Joyce Banda: Ndine okonzeka

Malinga ndi Bambo Andekuche Chanthunya amene amalankhulila mayi Banda, a Banda ati sachita mavuvu ndipo azipeleka kwa Apolisi akangopatsidwa chikalata chomwe bwalo linapeleka kuti awanjatile.

“Padakali pano, chikalata chomwe akuti adatenga ndipo chinawapatsa mphamvu Apolisi kuti akwizinge a Banda sanachilandile. Iwo angomva kwa anthu, koma akachilandila, akazipeleka okha ku Polisi,” anatelo a Chanthunya.

A Chanthunya anaonjezelapo kuti a Banda ndi munthu omvela malamulo ndipo kukhala kwawo kwa kunja si kuthawa milandu.

Apolisi anaulula ku mtundu wa a Malawi pa 31 Julaye kuti iwo ali ndi chikalata chowapatsa mphamvu zonjata mayi Banda pa nkhani yokhudzana ndi kusolola, ya kashigeti.

Apolisi anati anthu angapo anaulula kuti a Banda anachitapo gawo pa kusolola chuma cha boma.

Malipoti akuti a Banda padakali pano ali mu dziko la Amereka.

Advertisement

206 Comments

 1. Koma a malawi Tilankhule chipogwe paza ziiiiiii, anthuwa amagotigwilisa ntchito gati munda akunziwana tiyeni tigwire ntchito zinazi tinzigopenya

 2. akamtengenso bingu kumanda azamwereze pandalama zomwe zinapezeka mnyumba yakhe after atafa ndippamene azaweruze pp akufuna kungosangalatsa anthu pamene zamlepphereka kale ndi chitsiru peter

 3. Chilungamo chioneke. Malamulo agwile ntchito zimatheka bwanji munthu kuba foni ya nzako kumangidwa kuba Tomato kumangidwa kumenyana kumene kumangidwa kusiya nkazi kumene kumangidwa.iiiiiiiiiiiii Efe tikudikila kuti JB amangidwe basi .chifukwa ndikanakhala kuti ndalama zimenezi mwaba ndinu bwezi pano mili ku ndende. Tikunena pano anthu ena anaba Radio yeyeniyi ali ku ndende.Apolisi kumene muliko thamangani nsanga mukanjate JB .

 4. A d, pp atiuze ndramaza 92 million irikutu yachimanga yachaponda ndram zirikuti zangwiranjitoyanji jodialabungwe asiyajudufuza zaku dpp awadyesera amalawi timaopaboma muzibwerakuno ku jnon myzaonezimenezimachitika voma eimaipa andu andu saopaboma komaukatiuzuzure mutimumangeni zitsiruza aporisic nazizikutenga tiyangats mukumarimbanandimzanu tiuzeni 92 anaba a dpp irikuti

 5. Kaya amangidwa or ayi zisandikhudze ine ndikuvutikabe ndiunphawi mmene ndidabadwila sndidagwilepo ngakhale 20pin pakamodzi ndimangothela 5pin nde awo alindichuma kale sindingayankhuleko bola 2019 ndidza kavotabeso pa blue zinazi ai

 6. This is what we call stupidity of the stupid this is the game of devils.Where Malawi going asatana amenewa akufuna amalawi atani kodi?akufuna muvale ziguduli mkumaenda mu msewu kuti adziwe kuti zinthu siziri bwino.If i was very very rich ndikadangothana ndi uyo opanda manoyo mkumamalizira tinsabwe tinati.Abakha amenewa atikwana bwanji basi kumangodetsa madzi amati tidzimwa kuti? ku Theba?ku UK?ndisaname pakufunika luso lophera abakha apo biii tidzingomwa madzi amatope mpaka kale.

 7. Olo amange Ife tizapindulapo chani tiyeni tizingodya mpunga ku mpalombe basi aboma ndifiti zokha zokha onse ali kolamulako cashgate imawakhuza kod saziwa ndani tingotenga nazosabwi malemu matafale nati olakwa ndani palibe anayankha wamanga zake naeso azamangidwa ndithu

 8. What malawi will benefit after all, kodi kwacha ikwera mphamvu, nanga madzi aleka kutuluka ndi tudzi, nanga aphunzitsi salary adzakwera, nanga katundu adzatsika mtengo you promise us to develop malawi not to arrest someone or atati ndalamazo wapaleka mudzadyabe mbuzi inu and jb alibe problem izi zidayamba kalekale bola ndingola mulonda basi

 9. Panganizanu miranduyanu mwayibisa mukunamizira mzanu murungu akuranganichabe musatipusise ifeosaukafe sindizavotaso mpakamoyowanga kuribwino kumarimbanandizamoyowanga

 10. Zaziii Kumanga kwa 12hrs kenako belo mlandu 10yrs usanathe tinaonela chilumpha ndi muluzi up to day mlandu sumaoneka mutu wache

 11. 1995 police inatenga chikalata chomanga Kamuzu Banda olamula ali Bakili Muluzi 2015 police inatenga chikalata chomanga Bakili Muluzi olamula ali Bingu Muthalika,2013 police inatenga kalata yomanga Peter Muthalika olamula alu Joyce Banda ndipo 2017 police yatenga kalata yomanga Joyce Banda olamula ali Peter Muthalika lotani tikupita kuti?

 12. Vitsilu inu mukulimbana ndi zinthu zopanda phindu bwanji mutigule chimanga bwa kumangolengeza pama Radio koma pa ground ndalama Ku admarc kulibe shatapu

 13. Dilu PhwiPhwi paulendooo. Out of govt in 2019. Get ready to rotte in prison.

 14. mau ongozilimbisa mtima, alipo samaopa kumangidwa?. ena m’buyomu anangomva kuti talowani musungidwe mwakanthawi sanagwe, bp kudwala, koma analipo amuna ena analowa m’kukhalamo osatekeseka olo kudwala, mapeto ake mkuwatumizila madokotala kuti akabaye Jackson ngati akudwala mcholinga choti akangowamaliza kuti asazowese mtendele, lelo siizo kuthawa kwanu komwe akupeza wayamba kuzilimbisa mtima, ai, m’ene zimakhalila. amati ukatamba uziyang’ana Ku m’awa kuopa kungakuchele, ndiye kwachano.

 15. Ndizaimba hosana hosana nane ndizatenga masiku omwe azakhale ku nde nde ndikupita nawo kwa Jakobo Nzuma kukamuonesa ndikumufusa kuti ankaziwa ndani kuti azauvala bozankosi lelo wavala monga mmene anachitila #Bingu atamwalira nkhonya yobweza hahahahahahahaaaa ndizaimba #Hosana #Mwana wa #Davide

 16. M’chifukwa osaukafe tikungothawa dziko lathu lomwe chifukwa cha uchitsiru wa akulu akulu akumipando yawowa, ngati zikukukanikani bwanji kumasiya zinazi makamaka moyo opondeleza anzanuwu, akulimbana ndi mzawo m’mawa okuba ndiiwo

 17. Kodi olemba nkhani inu bwanj kugudwa mopusa kodi tili nanu mMalawi limodzi ngati a Malawi ,bwanj simufunsa za 1.7 bn ya Muluzi ,277 bn ya nduna 7 zija, 61 bn ya Bingu ija ,chitani manyazi ndi kukomeza za JB

 18. Mbava zokhazokha inu jb simungamumange munalephera kumumanga bwanji atangoba kumene??? mumaopa akachokapono muyambepo wachoka utaba tikumanga mukansaka kumpeza osamumanganso coz mukuziwa akuululilaniso zanu amangofuna azitiphumba mmaso andalewa amadyela limodz anthuwa ndi agalu amangotidyela osaukafe nkumatiphimba mmaso potinamiza kuti akuchitapo kanthu kumbali akusangalala limoz

 19. This is backward thinking, am not a fun of her but for our country to start spending more on cases like these that historically we all know it doesn’t go anywhere i.e. Bakili Muluzis case etc, I think this is just a ploy for our ruling party trying to divert attention from current political development that seem to have a negative one on DPP like the coming in of MIA into MCP that has for sure shaken the ruling party, every party is testing popularity by earlier than expected launch of the campaign period, like the DPP now see their popularity dropping, and is now using every tactic trying to draw attention from MIAs bouncing back to “government is doing enough on what happened to our monies ” please!!!!!

  1. So point yako ndi yoti munthu ngati waba kapena akumuganizira kuti waba azingomusiya basi eti?Kodi anthu inu munatani?Mmayesa pompano munkati Chaponda amangidwe inu?Kapena mukufuna azimangidwa a boma okha?

  2. Msaywale Nymbo Ya Lucius Kut Kubedwa Kwa Ndakama Mboma Linayamba Nd Mcp Kenako Udf,dpp,pp Apaso Mkuona Nokha Pitala Mmene Akuchtla.Asyen Azkangana Amaonamo Phindu

  3. Msaywale Nymbo Ya Lucius Kut Kubedwa Kwa Ndakama Mboma Linayamba Nd Mcp Kenako Udf,dpp,pp Apaso Mkuona Nokha Pitala Mmene Akuchtla.Asyen Azkangana Amaonamo Phindu

  4. James Tamani how long has it taken for our government to start this? With only a few months to a 2019 election campaign launch ? for it to come and start pushing on this, doesn’t it occur to you that this is another one of those wasted government tax payers in the offin as well?

  5. maiwa ndale analemphera kale.koma akayankhe milandu basi!maiko,mabungwe ndi amalawi akufuna kwabwino tisatira nkhaniyi bwino lomwe.

  6. alanda katundu wosalayo ndikumubweza ku boma ngati momwe boma linatengera press corporation kuchokera ku banja la kamuzu amafuna kuba.this is the era of e-economy whereby it very easy to freeze or trace properties(assets)

 20. 2019 yayandikila, mungofuna kuononga mbiri yozanu basi, mwayiwala zanuzi tsopano. musiyeni mzimayi ndalama aphuzitsileko adzukulu, misonkho amalawi akadakhoma mukabeko zanu.

 21. A dpp akuziwa kut 2019 yili pafup nde akufuna kufoylitslatu za amay aja, kut mwina azadutse moyera…koma nanga za m’bale wathu chaponda zli pat?

 22. Ndale zapanyasaland ndi bvala zilimbe, lero ndiiwo koma mmawa muxiwe kt xinkhala Kwa inu.anthu omwe mudawampha aja pa 20th July we are still counting including imfa ya Njaunju muxatiyankha. Nanga tikambe xa chimanganso ngati ?? ayi izo mukuziwa mkale osabvutika mkukuuzani.

 23. Ine ndingoyamika mayi abwele adzawone ana. Eishi kungoti ziii ngati osabeleka lol lol ngati imavuta transport mayi apa mwayi wapezeka .

 24. hehehe at ndrama zanga 😀 ..Dd u even notice kut bdrama zanu zabedwa?? kupanda kuululika mukanazwa kut akuberan ndrama 😀 …Hahaha ndale adha 😀 😀

 25. Osangobwerako bwanji, mpaka amadikira unyolo Kaye? Tabwerani mbava zofafana nthenga muzidzaulukira limodzi, Malawi ndi wanu uyu, muononga nokha osati osaukafe ai.

 26. This is political propaganda.they want to shun away on the hot issue of Chaponda.there is no justice for the rich in Malawi.musatinamize pangani za Chaponda ali ku Nyambadweyo.Malawi police is under armpit of DPP.they are being directed every step to go with this issue.Where shall we have an independent police service?Dzuka Malawi.

 27. palibe chanzelu chomwe ine nikuchiona apa chofunika nichakuti tikuyenera kuyang’ana chitsogolo pazaka 53 takhalazi osati kulimbana ndi mayiwa ayi cifukwa sikuti zinthu zisintha poti mwawamanga ayiii!!!!!!!!!!!!!!!!!!! lets focus on future

 28. akuti wakonzeka kumangidwa, manga pavutaso pati mmangeni ka nthawi, mungotionongetsa data bundle apa ine ndufuna ndinve kuti wamangidwa

 29. palibe cotipindulila ife amangde asamangidwe cimodzmodz ztithandza can ife guyz kt amumange ndende yake sngkhale ngt imene iwe nd ine titaba kmatu kuba cithu cocepa kuzuzika kwakeko kma iwowa kuba zoculuka ndende zolongosoka zot ar kundende osadzwika nde iwe nd ine tiye tzisiye nbare ameneyo asamangidwe musiyen dende

 30. My strong presdent…….dr joy banda…astill believe in your inocence….nomata how many people shall turn against you…truth will alwys come out…olo atakunyozani or kukupakani matope chotani…trust in God…he will fight you.

 31. Pamalawi panangochuluka kubwezerana pamapeto lake palibepo chitachitike kungowononga ndalama zathu APA….milandu yanu imatha kumalawi kuno?….

 32. aliyense atakhala presedent sangamalephere kusolora chisaipire JB oro mutakhala inu simungalephere kusolora even bwampiniyu akusolora panopa simungadziwe coz he is ruling koma akadzatuluka pansi udindo 2019 mpamene mudzadziwe kuti iyiyi ndisizinamtole

 33. Ndataya chikhulupiliro ndi atsogoleri andale. Ngati nchilungamo bwanji sanalande ndikubwezela ku boma ndalama pomwe zimapezeka ndi anthu zitabedwa kumene? Pano azidyaidya ndiye akufuna azitipwetekesa mutu ndikuwamvesela andalewa za ziiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiiii.

 34. Ah Kungomusia Coz Presiden t Aliese Amakhala Akutibera Ndalama Zanthu ,bakili Anaba, Bingu Anabaso , And Uyu Petala Muzamva Ngat Zinaamba Kale Za Chaponda Tikungotaa Nthawi Olo Atamunjata Abweza?

 35. ndilibe nthawi yopikisana ndi achuma popeza ndine mphawi chuma ndilinacho chodya ndi banja langa

  udakakhala wanzeru admn sukadalemba idzi dzana ndi dzuro tidamvapo boma likusakasaka chaponda pa maize gate mutamupedza mudamumanga nagonako 6hrs after that what next? ???? JB akagwidwa azakhalako 4hrs pamene chuma adya kale chasowapo ndiye phindu la ife osauka omwe sitili m’boma ndiloti chani pa nkhaniyi? ???? ndidakakhala oti ndili ku parliament bwezi maganizo anga mwawamva thesani ziphuphu mukuzionazo first before you go to JB abakili ndi aja adadya chuma what was next nkhaniyi simapitilila popeza ali pamkhathiyo nayeso akufuna ndalama let the money fight

  1. Hahahahahahaha Kumeneko Ndikuyakhula Kwa A Namalira Wamva #Aubrey, Bakili Atakumananazo Sanathawe, Kma May Anuo Akuthawanji? Eee Oyipa Anthawa Yekha, Nde Ndi Tme Yot Akusidwe Basi, Kkkk

  2. Aubrey Banda zina mwalankhula mwanzeru koma ukuti admin walakwisa pat kupanga post !!? any media imapanga post nkhan disregarding kut nkhaniyo ikuwakhudza osikuwakhudza kapena ndi olemera or osauka xo take note ov dat

  3. Mwaonat #Aubrey, Wa Chaponda Ndi Chaponda Wa Mayi wa Ndi Wa Mayi Basi Kmas Wa Masten Anu Watha 3yrs Kma Dr G Chaponda Ndi Chaka Chomwechinu Nde Mwat Bwanj? Nde Nde Nde Mukamba Man Smunat Kwasala Uladi Mussa

  4. Am not defending anyone ine ndungofuna enanu mchape mmanso akutsogolo asamakupusiseni kuchoka momwe Dr H kamuzu banda kufika lero and anthu angti asokoneza chuma chaboma ndipo ndi angati adagona kundende ngakhale 3 days inu anthu andalewa asamakuikeni masamba wakeup malawi tachuluka mbuli

  5. muziwe kuti zinthu zimasintha pang’opang’o.nthawi yoti pulezident aziteteza mbava zikuluzikulu ikutha.apa sizandale.amangidwe nanga mpaka kutyola bank yayikulu.tiyambira pa amai awa.there is direct evidence.

  1. akanayamba kubweza ndi Nduna zija zinakhuzidwa ndi K577 billion n’chifukwa chake nayo akuti sakunjenjemera ndi Unyolo wawo even Chaponda nayonso sanganjenjemere nazo dziko lathu lili pamavuto azaoneni

  2. palibe chomwe iwe ndine tingapeze zitayeni ngakhale iye atapereka ndalama m’mesa zilowabe matumba anthu ena iwe upindulapo chani????

Comments are closed.