Unyolo wa JB ulipo tsopano – atelo Apolisi

Advertisement
Joyce Banda

Patangotha masiku mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika atapempha kuti mtsogoleri opuma a Joyce Banda abwele, Apolisi nawo alengeza kuti akufuna kunjata mayi Banda.

Malinga ndi chikalata chimene asayinila Bambo James Kadadzera amene ndi mneneri wa Apolisi mu dziko muno, mayi Banda akufunidwa kuti azayankhe milandu ya cashgate.

Joyce Banda
Joyce Banda

“A Malawi ambiri mwakhala mukudabwa kuti nkhani imene anthu ena anatchula kuti amatumidwa ndi mayi Banda kuti asolole ili pati,” alemba motelo Apolisi.

“Tsopano tikufuna kukudziwitsani kuti tamaliza kafukufuku wathu okhudza mayiwa ndipo akuoneka kuti ali ndi mafunso angapo oti ayankhe,” chikalatacho chikutelo.

Apolisi ati m’mene iwo afika potelopo, tsopano ndi okonzeka kunjata mayi Banda.

“Tatenga chikalata chotipatsa mphamvu yoti tinjate mayi Banda ndi kuwasakasaka kumene ali kuti azayankhe mafunso,” atelo a Polisi.

A Banda anachoka mu dziko muno ataluza zisankho mu chaka cha 2014.

Chichokeleni sanapondeko kumudzi kuno ndipo mbiri ati iwo ali ku Amereka.

Mmbuyomu akhala akunena kuti akubwera koma mpaka lero kuli chete.

Sizikudziwika ngati mayiko amene akusunga a Banda ati awatumize ku Malawi kuzayankha milandu yawo.