Unyolo wa JB ulipo tsopano – atelo Apolisi

236

Patangotha masiku mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika atapempha kuti mtsogoleri opuma a Joyce Banda abwele, Apolisi nawo alengeza kuti akufuna kunjata mayi Banda.

Malinga ndi chikalata chimene asayinila Bambo James Kadadzera amene ndi mneneri wa Apolisi mu dziko muno, mayi Banda akufunidwa kuti azayankhe milandu ya cashgate.

Joyce Banda

Joyce Banda

“A Malawi ambiri mwakhala mukudabwa kuti nkhani imene anthu ena anatchula kuti amatumidwa ndi mayi Banda kuti asolole ili pati,” alemba motelo Apolisi.

“Tsopano tikufuna kukudziwitsani kuti tamaliza kafukufuku wathu okhudza mayiwa ndipo akuoneka kuti ali ndi mafunso angapo oti ayankhe,” chikalatacho chikutelo.

Apolisi ati m’mene iwo afika potelopo, tsopano ndi okonzeka kunjata mayi Banda.

“Tatenga chikalata chotipatsa mphamvu yoti tinjate mayi Banda ndi kuwasakasaka kumene ali kuti azayankhe mafunso,” atelo a Polisi.

A Banda anachoka mu dziko muno ataluza zisankho mu chaka cha 2014.

Chichokeleni sanapondeko kumudzi kuno ndipo mbiri ati iwo ali ku Amereka.

Mmbuyomu akhala akunena kuti akubwera koma mpaka lero kuli chete.

Sizikudziwika ngati mayiko amene akusunga a Banda ati awatumize ku Malawi kuzayankha milandu yawo.

Share.

236 Comments

 1. Kodi mayiyu waipalero ayambe afufuze ndalama yomwe adamangila ndata ija abwela liti abingu kt alemele choncho,muyamikeni mayi chaka chimodzi adakuwonjezelani malipiro kawiri yamikani.

 2. amalawi unachuluka ndi umbuli…very cheap.munthu samangidwa asanalowe khoti,akapezeka olakwa nobody is above the law SHE WILL BE ARRESTED.the current president is innocent for now.some of u guys are indeed being childish.ngati makolo anu anadya nawo dolayo mukonzeke kumakasiya za kudya ku penitentialy

 3. Tikulila ndalama zanthu za sonkho ife kumasamba opanda soap ngati simagwila Ntchito.nde alekelenji kumangidwa palibe mmalawi amene ali okondwa pazimene maiwa b ndi gulu lawo anachita.Mangidwani mai ulendo wa kundende wa bwino mulungu Akulangeni ndithu.

 4. NKHANI YAYIKULU

  Boma lililonse ndilokuba nde mot tindalama tilipoto agwilise mwanzelu km nkhan ndalama izingothera mumabwalo umenewo nde umbuli ngt malaw ndalama zachuluka bwanj osamangowathandiza anthu onsewa akuvutikawa km tizingomva zopoyira bas .Bakili adaba ndalama zaboma even kamuzu same Bingu same Amayi nawonso ndechavuta ndichan? Milandu yabakili ikuthandalama zambili kuma bwalo amilandu km kumangokakamira zaziiiiiiii .Asiyen may JB osamalimbana ndizinthu zopita kale pomwenso zikusakaza ndalama zaboma .kuli maophaz care ambili omwe akusowa zithandizo km kumangokokana zaziiiii malaw zizachita bwino chifukwa cholimbana ndizinthu zopanda phinu .boma lililonse ndilokuba tiyen tiziyang’ana zakusogolo osat zambuyo ndizopita tikatero malaw tizachita bwino (Palibe wabwino )

 5. Mam musabwele dziusani asakuvuteni awa zanu zinaela kale awanso kuno akutinzunza kuno naonso akuba kuno iwo asakhale ngati angelo kuba kunayamba kalekale kamuzu bakili bingu peter chaponda nduna zambili ma mp ma cansala ndiena ambili musade nkhawa mayi imwani khofi ku america

 6. Mam musabwele dziusani asakuvuteni awa zanu zinaela kale awanso kuno akutinzunza kuno naonso akuba kuno iwo asakhale ngati angelo kuba kunayamba kalekale kamuzu bakili bingu peter chaponda nduna zambili ma mp ma cansala ndiena ambili musade nkhawa mayi imwani khofi ku america

 7. Mbamva zikamaba umagwira yemwe wampenzayo sumalimbana nd munthu osangwira ndye mmai amenei mangidwe basi wadziwika ku adatchyola lock wa ndalama nd ameneyu adachitaso kumujam bula pa malaya atatchola umboni ulipo

 8. kukhuta soya pieces basi ndemwati mnkhuto wanuwo i want the former president to return home hhhhhhhhh koma abwana amenewa mmalo momumanga chaponda afuna kuwayamba kaye adan? nazoso mbuzizo mkumati unyolo wa jb ulipo kkkkkkkk answer upolisi wake uti?

 9. Mmmh mwaona kt nthaw yasar yochepa nde bas muzivute nde mukufuna mundiuze kt peter sadadyepo ndalama za boma pot fuel akuchoka paife nde ngt amai adachosapo ndalama alekeni kod nthawi yonse ija mudar kut kut mpaka muziwauza kut abwere nawe iwe wa police mwapeza mpata pot przdent walowapo nde nyomi nyomi kod kithakhar kut Dpp yazagwa kod mungatani kod zanu zija zomwe mukubisa sizizaululika kod nanga ifa za athu ngt mfana uja wa school uja mesa mudapondeleza cz ndi nkulu wanu adapanga zonse kd chulungamo mumafuna kt chizafike pat nyasssss

 10. khani ndiyoti amangidwe akayakhe mafuso kodi bakili mukunenayo mesa nayeso khani yake ilipo ndipo azayakha komaso mukuziwa kuti bakili ndimatenda amsana aja ikatulu kalata yofuna kuti akayakhe ake mafuso muzava kuti dokotala akumufuna kunja klklk

 11. Atsogoleli apamalawi kuba basi,amuluzi anaba,abingu anaba,amayi anaba awaso awa alipowa nawoso akusolola,mind you God is watching,malawi shall never develop if our leaders will not change,kulira kwamuthu wakumudzi mulungu akumva,muzilandira zilango modzimozi.

 12. Mwasowa zopanga a Dpp instead of fixing mavuto azachuma alipowa nkulimbana ndikumanga anthu, you are bizy digging old cack, focus on our things. Watch this iweso tizakumanga ukazachoka pa mpando en thats a time you will feel the same pain.

 13. Ndale zakumalawi all the leaders we vote into power end up embezzling the money from donors intended to help poor malawians, please our leaders God is watching

 14. Polowa Boma ndikutuluka ndipamene amapeza mwai wakuba,Kamuzu potuluka Boma adaba naye Muluzi adangokafikila kutapapo, a DPP potuluka Boma adaba Joyce Banda naye adangokafikila kutapapo potuluka adabaso,DPP polowa idangokafila kuba kukwatisa maukwati,5yrs yomaliza ulamulilo wa Muluzi adapha mwana wa sukulu ,ulamulilo wa Bingu adaphaso mwana wa sukulu palibe adaimbidwa mlandu ,I Wadi adachosedwa ntchito chifukwa chofuna kumuimba mlandu Muluzi .Ife zosowa zathu sizomangana zanuzo mudalonjeza muzapanga chani zatheka zomwe mudalonjeza

 15. Asabwele a joyce bandá ñaoso apeter asowa zochita thàwi yoseija osamuitànisa akamutañe paño?àķufunà amuipisiĺe cv mzaoyoooooo.sithawi yakampeni ikuyandikila.inu mukuoná bwaaaaa!!!!

 16. Zandale Zokhazokha Kukhala Mmalawi Mkulimba Mtima Akuba Nose Mbuzi Azitsogoleri Ose Mbuzi Pita Mbuzi Chaponda Mbuzi Zikutiwawa Mmalomonthandiza Anthu Mukudzilemeretsa Nokha Pamtundu Panu A DPP Mwava?

 17. corruption pa Malawi ndie kudya kwawo even peter mukumunenayo mukuziwa komwe akusunga ndrama zobera dziko? kungoluza peter this s round muzamuona sazakhala kumalawi azizapita kwao komwenso Ali ndi Green card ID

 18. palibe Ku mW anamangidwa chifukwa waba ndalama za boma ayi kma wakuba zovala ndiye tiyeni timuwoche were guyz ziku pwetekesani mutu iyiiiii ndi goverment mission panja imadya pamene ayimangilila amw azanga tiyeni tisekule maso amw tiyeni tilibike kungwila ntchito kuti ana sakhale ndi njala

 19. Koma Amai anaba mowonetsera kwambiri ndi mwana emwe kuchita kuziwa achina bakili ndi bingu amaba koma fans simadziwa koma Amai anaonetsa kuti ndiamayidi….

 20. What a rubish gvt. Instead of initiating development projects in the country wasting time with the former president. Malawians are not after that , pItAlA be wise! Fight the current corruption scandles. why blindfold Malawians?

 21. Asowa chochita alakwanji jb apolice ndinu zitsilu pamozi ndi munthalika ngati mufuna kumanga bwanji mutamanga chaponda mbava yeniyeni,munthalika kuntha mano mukamwa ndi zelu zomwe fuck you stupid wali

 22. musaiwale kut pamene mulipo ena akubweraposo muzalira nanu ndikuba kwanuku inu mukulimbana ndi mayiwa bwanji amene angakugweseni simayiwa ayi akubwerapo chakwera mbunzi za anthu. inu.

 23. pakut nd malamulo a dziko koma cholinga ndichakut abweze ndalamazo kapena kungozunzana chabe!? naga mukut a pita muthalika anawaitsnisa kut azayankhe muland! kapena anawaitanila zao ndikudabwa inu apolis mukut mwatengelapo mwai onjata amaiwa ndiye kut mwagwilizana nd bwanao titelo kkkkkkk inuso ndiye mbava zokhazokha manyaz bwa hahahahahaha

 24. If u have tried to open account but u failed, and u still want to have account don’t worry, am here to help u just call/WhatsApp on 0604945171. No need Work permit. No need Proof of address. We based in Capetown

 25. Ndrama zomwe mukufuna kukamangira Joyce banda chonde chonde wonjezerani ma salary a apolisi kapena gulani ma jombo amasoja kamba koti milandu ya corruption kumalawi siimatha nanga Bakili muluzi boma linawononga ndrama zingati

 26. jb is not coming to Malawi she will stay outside the country until Peter and his DPP come out of power, bingu anaba ndalama wamanga ndata bakili anabaso bwanji kulimbana ndi mayi banda gulisani ndata ndiposo mangani muluzi and then arrest banda don’t jump bcoz she is a woman

 27. Which is which. The president said she is not going to arrest her.Now the police says they have warrant of arrest. Malawi is very confused state.

 28. Si zonyengelera apa. Si zandalenso apa. Okuba nkhuku ndie amangidwe?? Akapezeka olakwa amangidwe basi. Amathawa chani?? Wakoma lero?? Chifukwa ali kuja ndie basi akumulakwira?? Abwere basi. Lamulo lisaka ukalipalamula. Si zolowesapo ndale apa wapalamula walalamula basi

 29. She was our mother ,amene sanachimwepo ayambe kumugenda miyala mkaziu kkkkk. palibe angamange mai ake or utakhalakuti unasainira polowa tchitoyo she Will remain our mother forever.Ngati sititha kukhululuka ndipovuta kuti Mulungu azatikhululukirenso.

 30. Kkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkkwidzingani

 31. Amusiye asamumange , ngati atamange then Nkhalamba Bakili Muluzi amangidweso chifukwa zonsezi ndiyeyu adalephera kuphunzitsa anthu za mfundo zabwino za Democracy

Leave a Reply