Kongeresi inazolowela kuluza ndipo 2019 tiyitibulanso – watelo Mutharika

Advertisement
President Mutharika

Mtsogoleri wa dziko lino amenenso ndi mtsogoleri wa chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) wati chipani chotsutsa cha Kongeresi chinazolowela kugonja pa chisankho.

Mutharika ananena izi ku nyumba ya boma mu mzinda wa Lilongwe pamene chipani chake chinakonza mgonero.

President Mutharika
Mutharika: Kongeresi tiyitibulanso 2019

A Mutharika polankhula kwa otsatira chipani chawo ananena kuti iwo ndi chipani chawo apambananso chisankho cha 2019.

“Ikafika 2019, wina asakunamizeni iyayi, tikupambana chisankho,” anatelo a Mutharika.

Iwo anati chipani chawo chilimbika ndi kuchita kampeni mwa khama ndipo pamapeto pake azapambana.

“A Kongeresi musawaope, aja ndi olephela basi. Chimene amadziwa ndi kulila kuti abeledwa chisankho. Alilanso 2019.”

“Paja 1999 analira kuti abeledwa. 2004 analilanso. 2009 chimodzi-modzi. 2014 analilanso, muwaona 2019 akulilanso kuti abeledwa,” anatelo a Mutharika.