Gulitsani zimenezi – a bwalo agangalama, ati nyumba ya Mphwiyo ipitebe pa msika basi

Advertisement
Paul Mphwiyo

Ngati mumakhala mukufunafuna mwayi wa nyumba ku Area 43 anaimba Tay Grin kuja ndiye sunthirani pafupi. Ndi kutheka mayankho anu muwapeza pano. A bwalo ati nyumba ya a Paul Mphwiyo ilandidwe ndithu.

Oweruza milandu wa ku bwalo lalikulu Mayi Ruth Chinangwa akana kuchitira chisoni mkazi wa Paul Mphwiyo amene amafuna kuti bwalo liyimitse kaye kuwalanda nyumba. Mwezi watha bwalo la milandu linalamula kuti nyumba ya a Mphwiyo ya ku 43 iperekedwe ku boma ati kamba koti mkuluyu adathawa chigamulo.

Koma atalandira chikalata choti asamuke pofika pamapeto pa Mwezi uno, Mayi Mphwiyo adathamangira ku bwalo komweko kukatenga chiletso. Mwa zina, iwo amafuna kuti a bwalo aunikenso ngati ndi koyenera kuti alandidwe nyumba.

Iwo amapemphanso ku bwalo kuti pamene akuwunikapo, iwo ndi banja lawo apitirize kukhala mnyumbamo.

Koma oweruza milandu a Ruth Chinangwa ati zimene anapempha ku bwalo Mayi Thandizo Mphwiyo ndi zachibwana chabe.

“Khoti lino liribe mphamvu yokazimanga yokha. Tinalamula kale kuti nyumba imeneyo itengedwe ndipo tsopano yapita ku boma basi,” chigamulo chawo titha kuchitanthauzira motero.

Malinga ndi bungwe lothana ndi katangale la ACB, chigamulochi chikutanthauza kuti nyumbayi idakali m’manja mwa boma.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.