Chakwera ndi samva mnkunkhu – Chatinkha

Advertisement
Lazarous Chakwera

Mmodzi mwa anthu odziwika bwino otsatira chipani chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) Mai Chatinkha Chidzanja Nkhoma adzudzula mtsogoleri wa chipanichi kuti mdiosamva za amzake.

Mai Chidzanja Nkhoma ati kusamva kwa mtsogoleri wawoyo a Lazarus Chakwera ndikomweso kwayambitsa mikangano yokhudza kuitanitsidwa kwa msonkhano waukulu wa komveshoni wa chipanichi.

Chatinkha Chidzanja Nkhoma
Chatinkha Chidzanja Nkhoma athila nkhondo a Chakwera.

Mai Chatinkha amalankhula izi munkucheza kwawo pa lamya ya mmanja ndi mmodzi mwa aphungu anyumba yamalamulo wa chipanichi a Lingson Belekanyama.

Mmacheza awo omwe afalitsidwa kwambiri pa watsiapu, maiwa anati kukangana mumchipanichi inayamba kamba koti a Chakwera akutemetsa nkhwangwa pamwala kuti sangabwezeretse mmaudindo anthu omwe anawachotsa.

“Vuto ndilakuti Chakwera samamva zamzake ndiposo samafuna kulemekeza maganizo amzake, ndipo zonse zikuchitika panozi sizinakachitika achikhala kuti amamva zaamzake.

Ngati mukukumbuka bwino, nditauzidwa kuti ndinene zomwe ndikufuna ndinati ndikufuna anthu one omwe anachotsedwa kuti abwezeretsedwe mmaudindo awo omwe anasankhidwa pa komveshoni yapitayi.” Anatero Mai Chidzanja Nkhoma.

Iwo anauza a Belekanyama kuti chipani chawo chitha kuchita bwino ngati mtsogoleri wawoyu a Chakweraatayamba kumva maganizo a anthu ena. Ndipo anati mmalo mwake mtsogoleri wawoyu akupanga kuthekera kuti chipanichi chizamukondebe ngati msonkhano wa komveshoni.

A Belekanyama omwe amaoneka kuti nawoso akufuna kuti komveshoni yomwe ikukambidwayi itachitika anauza a Chatinkha kuti anthu otsatira chipanichi akuenera asakhale ndiphuma pankhani yomwe ilimkamwamkamwa yokhudza.

Nkhani yonse yokhudza mikangano ya komveshoni inayamba ndi mulembe wa chipanichi a Gustave Kaliwo omwe paokha ndi otsatira ena achipanichi analengeza kuti chipanichi chikhala ndi komveshoni mwezi wa July a Chakwera asakudziwa kanthu kalikonse.

Tikukamba pano, a Chakwera anakatenga chiletso Ku bwalo lozenga milandu kuti mumchipanichi musakhale msonkhano wa komveshoni omwe unaitanitsidwa ndi a Kaliwo.