Chakwera ndi samva mnkunkhu – Chatinkha

145

Mmodzi mwa anthu odziwika bwino otsatira chipani chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) Mai Chatinkha Chidzanja Nkhoma adzudzula mtsogoleri wa chipanichi kuti mdiosamva za amzake.

Mai Chidzanja Nkhoma ati kusamva kwa mtsogoleri wawoyo a Lazarus Chakwera ndikomweso kwayambitsa mikangano yokhudza kuitanitsidwa kwa msonkhano waukulu wa komveshoni wa chipanichi.

Chatinkha Chidzanja Nkhoma

Chatinkha Chidzanja Nkhoma athila nkhondo a Chakwera.

Mai Chatinkha amalankhula izi munkucheza kwawo pa lamya ya mmanja ndi mmodzi mwa aphungu anyumba yamalamulo wa chipanichi a Lingson Belekanyama.

Mmacheza awo omwe afalitsidwa kwambiri pa watsiapu, maiwa anati kukangana mumchipanichi inayamba kamba koti a Chakwera akutemetsa nkhwangwa pamwala kuti sangabwezeretse mmaudindo anthu omwe anawachotsa.

“Vuto ndilakuti Chakwera samamva zamzake ndiposo samafuna kulemekeza maganizo amzake, ndipo zonse zikuchitika panozi sizinakachitika achikhala kuti amamva zaamzake.

Ngati mukukumbuka bwino, nditauzidwa kuti ndinene zomwe ndikufuna ndinati ndikufuna anthu one omwe anachotsedwa kuti abwezeretsedwe mmaudindo awo omwe anasankhidwa pa komveshoni yapitayi.” Anatero Mai Chidzanja Nkhoma.

Iwo anauza a Belekanyama kuti chipani chawo chitha kuchita bwino ngati mtsogoleri wawoyu a Chakweraatayamba kumva maganizo a anthu ena. Ndipo anati mmalo mwake mtsogoleri wawoyu akupanga kuthekera kuti chipanichi chizamukondebe ngati msonkhano wa komveshoni.

A Belekanyama omwe amaoneka kuti nawoso akufuna kuti komveshoni yomwe ikukambidwayi itachitika anauza a Chatinkha kuti anthu otsatira chipanichi akuenera asakhale ndiphuma pankhani yomwe ilimkamwamkamwa yokhudza.

Nkhani yonse yokhudza mikangano ya komveshoni inayamba ndi mulembe wa chipanichi a Gustave Kaliwo omwe paokha ndi otsatira ena achipanichi analengeza kuti chipanichi chikhala ndi komveshoni mwezi wa July a Chakwera asakudziwa kanthu kalikonse.

Tikukamba pano, a Chakwera anakatenga chiletso Ku bwalo lozenga milandu kuti mumchipanichi musakhale msonkhano wa komveshoni omwe unaitanitsidwa ndi a Kaliwo.

Share.

145 Comments

 1. Ngati maganizo ndioti chipani cha a Gogo tipala. Agogo anachoka. MCP ndi chipani chokhacho chime ndi cha AMalawi.Zinazi ndi za achimwene, a bamboo kapena cha Amati. Choncho Mayi mukanadekha.

 2. komadi tiwoneko chakwela mwina tiwoneko zina ndakhala ndiku votela chipani changa cha DPP koma akungaba 2019 ndidzawone chakwelayu mwina tiwoneko Ku sintha

 3. Amene amuyandikila ndiomwe anganene zenizeni za dr cakwele osati inu akharupa asakhwi mungolankhula pamene simunakhele nao pamozi mumangowaona mmanyuzi kapea mmawailesi simungaone colakwika

 4. Zomwe akupanga cha Chakwerazi anaziyambita ku galileya (ku assembless of god) busa wa chinyengo kusamva kumeneku ndiye azamva zonena za amalawi akazawina? Mundiyankhe inu masapota a puludzu inu

 5. Enafe timadziwa kale kuti mmene convention imene amayitanisa mzake uja in wat was their plan B, then she would start talking nonsense against Chakwera again! Musiyeni ndi magazine ake a blue! Zonse ndi nthawi!

 6. Ndimaona ngati Mai chatinkha mukanakhala Kaye pheee mukulakwisatu inu ndipo musachite zinthu ngati kuti inuyo mungatsogolele chipanichi Akutumaniwo akulakwitsani mwamva

 7. Mai Chatikha ndi modzi mwa anthu oziwika mu chipani chimenechi. Ngati akudabwa ndi zochita yudasi Chakwera sakunama. Ndiye ena inu mukamati Chakwera boma muli mbuuuuuu pamene amene amadyererawo akudabwa ndi zochita za Chakwera. Musathamange kumanyoza munthu ngati inu amakuziwani a chipaniwo.MCP kuwina lero amutenga Chatikha ndikumupasa mpando wabwino inu mukudya gaga ndi banja lanu mphuno ili biiiiiiiiii

 8. ukamalinbana ndi amisala palibe kusiyani nonse ndi amisala …… INE NDILIBE CHIPANI NDIPO POMWE NDILI INE KULINBANA NDICHIPANI NDITAYA NTHAWI YANGA ….. MUZIPANGA ZANUZIMENEZO …. ZAZIIIII NO SOAT …. SIMUZIWA AGALU ANDALEWA AMAKUYESANI NYANBO

 9. Mungatani mungatani ine nga nga nga nga pa Chakwera amene simukufuna chakwera ingotulukani mukayambitse chanu chipani, nkholokolo akutumani akuppwrteketsani,

 10. ine siwandale ndipo ndilibe chipani chili chonse pa dziko la pansi koma langa ndi pempho kwa m’zimaiyu kuti mwai alinawo akhoza kungoyambitsa chipani chake kusiyana ndikumakhalira kunyoza chosecho amvala makaka ofanana

  • Ai sichoncho, musaweluze motelomo, maiiyo simulendo, osokoneza ndi uyu muti m’busayu maiyu ndi landlodie, mkului uyu m’busai ndi tenanti aaaaa mukuganiza bwaaaa.

  • Cytonie ulibe nzelu ndakuona choncho kodi mayi Chatinkha mchifukwa chani nthawi zonse amakhala busy ndi Chakwela? Bwanji ngati akufuna utsogoleri osangoyambitsa chipani chake

  • ndanena kale ine siwandale koma amaiwa nthawi zonse ndikamawelenga zoyankhula zawo zimakhala zonyoza chakwela ndiye pa chichewa pali mau oti chikuni ukachiwona kuti ndi chomwe chikupanga utsi kwambiri umangochisolora tsono poti uyu mzimayiyu ndi munthu ayi kaya sanachedwe angochokamo ndiyeyu basi mkukayamba kuphika zake ndizosabvutatu izi palibeso angadabwe ayi sinanga wathawa kumsamva kwa chakwela eyetu

  • cryton,MCP sichipani cha banja ngati mmene ili dipipi ndi udf nop,ndye chatinkha sangakhale landlord ngati chipanicho ndichake ayii,after all ndizimayi wolephera kale,kungoti chomwe chavita ndichakuti MCP panopa iri very strong moti ambiri sakugona nayo akungotsekula mmimda mwakamwazi,makadeti mitu yawo yasokonekera coz propaganda yawo ndimene ikupangitsa chakwera to be popular,hence no wonder ndi comment yanuyi…but coz its ur opinion ayi we respect it,kkkkkkk

  • #aCassim ndinu a Mcp musaputsitse an2..izi Ndi ndale & kuli ufulu wakulakhura kunjaku..akuyenera kudzudzura ngati Pena pake sakupaona bwino mopanda kummanga Nyakula wina kapena kukamponya ku Ng’ona….

  • Akanakhala kuti mayi uyu ndiwanzeru zakuti angayendetse chipani akanamusankha iye kuti akhale president wa MCP. Koma Mai uyu ndi madeya odyetsa nkhumba basi akhala choncho ndi mwano wakewo.

  • #shoaib undikhulupilire ine sindimayima pa mzere kukabvotela munthu ndipo sindingachite komaso sindidzapanga zimenezo koma ndimangowafunila zabwino amaiwa kuti mtima wawo usamakhale okhumudwa nthawi zonse chifukwa cha chakwela akhoza kufa ndi bp bola atangoyamba zawo ndipotu anthu akhoza kuwabvotela chifukwa akuwonetsa kuti ndiwolimba mtima mumayankhulidwe awo nanga mpaka kumunena mtsogoleri wawo kuti ndi gung’ungu’u iwo ndiye adzakhala ndani kweni kweni

  • chimene chimasiyanitsa dpp ndi zipani zina ndi kusakangana okhaokha openly. Ndipo ngati zipan zina ndi mzika za ku opposition ndi chifukwa choti zilibe direction ya umodzi mchipani, ndipo kukanganaku kumabweretsa zibowo nthawi yamavot. Dpp ilibe economic and social leaderships but political leadership. Udf idachuluka social leadership. Mcp idali good p economic leadership koma social and political leadership mmmm mbola. Mavuto a mcp pano akuonetsa kut president ndi omutsata ndi aphuma situational judgment ndyowavuta and ali nd false hope. a dpp ali ndi vuto lokhulupirira zawo zokha koma party and political organization excellent

  • @shadreck banda: zaonetsa kuti sumadziwa tanthauzo la excellent kuti kodi amapelekedwa pa zinthu zotani, ngati Dpp adaba ndipo akuba ndalama zaboma komaso alikupha anthu ngati Njaunju, Mbendela, Chasowa, kutseka chanco komaso kumenya ana aprimary kamba kakuti akuumiliza boma kuti lipeleke ndalama kwa aphuzitsi kuti anawo ayambe kuphuzira ndiye choncho pali chifukwa yowayamikila kuti zilibwino ndipo excellent?

Leave a Reply