Osewera anaiwalidwa uja wabwereraso Ku Bullets

Advertisement
Chiukepo Msowoya

Imodzi mwa matimu osewera mpira mdziko muno ya Nyasa Big Bullets ili ndichifukwa chomwemwetera ndiso kulumphalumpha italandiraso osewera wawo wakale, Chiukepo Msowoya yemwe amatumikra Ku Jubeki.

Msowoya yemwe watikitira mgwirizano wazaka ziwiri ndi timuyi msabatayi, wafika mdziko muno mgwirizano wake ndi timu ya Golden Arrows yomwe amatumikira utafika kumapeto.

Chiukepo Msowoya
Chiukepo Msowoya (Pakati) wabwereranso ku Bullets.

Ku Golden Arrows mnyamatayu anatikitira mgwirizano wa miyezi isanu ndi umodzi (6) komwe sanachite bwino kwenikweni.

Ngakhale Chiukepo amadziwika ndiukatswiri wake ochinya zigoli, mnyamatayu pamiyezi isanu ndiumodzi komaso pa masewera asanu ndi amodzi omwe wasewera ku Golden Arrows sanachinyepo mgolo la adani mpaka wabwera kuno kumudzi.

Chigoli chomwe anthu anachiona cha katswiri osewera kutsogoloyu chinali chomwe anachinya timu yake yomwe mmasewero ake oyambilira omwe timu yake ya Arrows inagonjetsedwa 5 – 2 ndi timu ya SuperSport United mu mchikho cha Absa premiership.

Ikakuona litsiro siikata, katswiriyu yemwe anthu ambiri kumudzi kuno anamuiwara, kupatula kuchinya timu yake yomwe anatulutsidwaposo m’bwalo laza masewero atalandira khadi lofiira pamasewero omwe timu yake imasewera ndi timu ya Bloemfontein Celtic.

Ngakhale mkuluyu sanachite bwino mdziko la enili, pali chiyembekezo kuti katswiriyu athandiza timu ya Big Bullets yomwe nayoso ili pa chilala chogoletsa zigoli.

Chiyembekezo choti Bullets itha kuyamba kuchita bwinochi chadza kamba koti timuyi yapezaso osewera wina wa pamwamba, Nelson Kangunje yemwe amasewera mpira mutimu ya Costol do Sol ya mdziko la Mozambique

Pa masewera asanu omwe Bullets yasewera muzikho ziwiri, TNM Super League ndiposo Chikho cha Airtel Top 8 cup yagolotsa zigoli zitatu zokha ndi timu ya Civo Sporting Club sabata yatha chikho cha TNM.

Advertisement

One Comment

  1. mbewa zikatha amanona ndi aswiswili, munthuyu anatha kale mulila naye nkuphonya ngat nzake uja chikaphonya sulumba kkkkkkkkkkkkk ine mawa pa bingu kukatenga cup ha heeeee mighty ndi dillu

Comments are closed.