Mavuto a Bullets apha Mfumu: sapota anakomoka ndi chigoli chokanidwa cha Siliva, wapitilira

Bullets vs Tigers

Wochemelera timu ya Nyasa Big Bullets m’boma la Thyolo watisiya pamene timu yake idachinyisa chigoli ndi timu ya Silver Strikers mu chikho cha Airtel Top 8 ku Mulanje sabata lathali, ngakhale kuti chigolicho chidakanidwa.

Mkuluyu yemwe anali Mfumu Lipulo mu boma la Thyolo anamwalira Lamulungu lapitali pomwe osewera wa Silver, Green Harawa, anamwetsa chigoli ali pamalo olakwika (offside).

Bullets imayenera kugoletsa zigoli ziwiri ndinso kuonetsetsa kuti asamwetse kamba koti timu ya Silver idali itapamantha Bullets ku Lilongwe 1-0 mu masewero oyamba.

Komabe, masewerowa sanatuluse chigoli chilichonse koma chigoli chokanidwachi sichidafike ndi uthenga wa bwino kwa a Lipulo.

Malingana ndi a Linos Phiri omwe amawaziwa a mfumu wa, lamulungu atachoka ku tchalichi cha katolika cha AAdololata, a Lipulo adapita kunyumba kwawo kumadikilira kuti amvetsele masewerowa pa wailesi.

”Amatsatila masewerawo pa wailesi ndipo zinalidi zokhumudwisa kuti Bullets simagoletsa. Iwowo adagwa pansi pamene olengeza mpira pa wailesi atanena kuti Silver yagolesa ndipo mmene amazanena kuti chigolicho chidakanidwa mkuti mkuluyu akatagwa kale pansi ndi kukoma, “ adatero a Phiri.

Ku chipatala cha Thyolo komwe anatengeredwa ndikomwe adauzidwa kuti mkuluyu wamwalila. Mkuluyu walowa mmanda dzulo.

Timu ya Bullets sidagolese chigoli mu masewera anayi yomwe yasewera.

Silver Striekrs yafikano mu ma semifinolo a chikhochi ndipo ikumana ndi timu ya Kamuzu Barracks pamene Be Forward Wanderers ipalana mamba ndi Moyale Barracks.

 

Advertisement

82 Comments

 1. My fellow Malawians u need to agree with me whether you like it or not. Malawi teams should stop playing football. Because all they do all times is loose.

 2. 360mins osachinya olo cha offside! pepani masapota + timu ya bb! ife(a silver) sitili moesa chaka chino! ndipo ma ref mu top8 anaesetsa kukukonderani.nafeso(a silva) sitili okondwa pomatikanira chigoli kawiri kose(home$away) tsono muonere matimu amzanu momwe akusewelera mu semi.

 3. Kkkkkkk iiiii koma ndiyetu chigoli chimoz mpaka kufa anthu awir. Ndiye mwasalanu ganizan bwino kusintha Chanel apo biii nonse mutha phsyitiiiii !!!!!! Coz BB ndiye izingoluzabe.

  1. Hiiiii kkkkkk iwe waziiwala khalidwe lako neba? Unakakhala kut siumatokota tinakakhala chete koma tikufuna tiphwese bas

 4. Im wanderers fan …this just the opinions not facts …coz munthuyu sikut anakamba nd pakamwa pake kut nd chigol coz anthu anangodziwa kut amavera mpira ….I hate danger left winger mukazavera interview yake sikut nd munthu adanena zimenezo koma Mr Gondwa ndiamene anamufusa kut “Kapena tinene kut ndi chigol cha silver chinachitsa kut bp ikwere?” so you see the question sikut nd munthuyo ananena zimenezo koma ntolankhan …mmmm zinaz ay mabodza bas kusadziwa kufusa mafuso kumeneko.

 5. Kkkkkkkk Koma Times Radio, & Dager Left Winger, Williams Godwa Achimwene Aakulu ! ! ! Kkkkkkkk Pepani Mapale Koma Muziziwakuti Zibwana Zanuzo Muphanazo Anthu.
  Timu Mpaka 6 hrs Osachinya Olo Cha Off Side Ngati AMasewera Atamwa Midoli Kkkkkkkkk

 6. ndye mwat mfumu??? kumwalila? nd off side goes ause mu tendere ndye iwe gilin harawa usanamenye short pa golo uziona upha nazo

 7. sibwino kuyankhula motumbwa choncho ayi aliyense adzafa kodi zikanachitikila m’bale wako ena mkumanyoza choncho ungamve bwanji, zamasewera tipange zamasewera zachisoni tipangenso zachisoni dzimvele ntolo.

  1. inde tizafa koma osati ifa yake ya bullets yi apo ndiye wanama akanakhala mfumu wabzeru bwezi akusapota Manoma the blues

 8. Tsiku Lake Lakwana, Draft Yokha Yakufa Kwake Ndiyo Ikupangisa Anthu Kulankhula Ngat Aduka Mitu Apai Koma Mwini Moyo Ankaziwa Kut Akuluwa Azafa Motelemu. Nanga Iwe?

 9. team ya nyasa bb izingomphabe masuppotar chocho mpaka onse kutha kt “peeeee’cuz chmemecho ndchiyambi chabe mpaka izafika ma ma sub kumasapota cuz of there bad resuits

 10. Mabanja asokonezeka, mabizinezi avuta, matenda sakuchilitsidwa, anthu akungomwalira. Zosezi chifukwa cha Nyasa BB. Eeeeeeeeeeeeeee!! Napepe

 11. Koma ngati anthuwa kumandako amafusana kuti “inu mwamwalira chifukwa chiyani, a mfumu amenewa akayankha zoona? Ndie pamwambo wamalilowo amati chawapha a mfumuwo ndichani?

 12. Eeeeee chakachino manda adzadzatu ndima supporter a MAHULE FC, Oooops! sorry MAULE FC chifukwa kuluza kukanapitilira. Boma lingolesa masapota onse a CHINKHOMA FC’wa kuti asamapite kumabwalo amasewero or kumvera mpira pa wailesi pomwe LIPIPA FC ikusewera game yawo coz BP ikupha anthu ambiri a ZIKWANJE FC.

Comments are closed.