FAM isefa ma bwalo osewelera mpira chaka chino, Blantyre yatsala ndi bwalo limodzi

Advertisement
Kamuzu Stadium

Bugwe loyang’anira masewera a mpira wa myendo muno m’malawi la Football Association of Malawi(FAM) lasefa ma bwalo osewerera mpira wa super league chaka chino.

Bungweli lomwe lalamulanso kuti bwalo la zamasewera lalikulu la Kamuzu ku Blantyre lisiye kugwira ntchito, lapereka m’dandanda wa ma bwalo omwe ndi okwanira kuti atha kusewerera mpira wa ligi chaka chino.

M’malingana ndi chikalata chomwe Malawi24 yapeza chotsimikizidwa ndi mlembi wamkulu wa FAM a Alfred Gunda mabwalo 12 okha m’malawi muno ndi amene FAM yavomereza kuti atha kupangitsa masewero akayamba.

Malingana ndi FAM pa mabwalo onse 14 omwe adayendera zaonetsa kuti mzinda waukulu wa Blantyre ndi bwalo limodzi lokha lomwe ndi loyenera pomwe ku Lilongwe mabwalo onse avomerezedwa.

Malingana ndi chikalatachi mabwalowa omwe ndi a Mzuzu, Chitowe, Nankhaka, Silver, Civo, Dedza, Bingu, Balaka, zomba community centre, Chilomoni, Mulanje ndi Kalulu ndi okhawo omwe FAM yaloleza.

“Izi zachitika potsatila ndondomeko yoyendera ma bwalo a mpira mogwilizana ndi a SULOM “(This follows a joint stadium inspection by the association and super league of Malawi (SULOM) in march and April this year) chatero chikalatacho.

FAM yatseketsa bwalo la Kamuzu pofuna kupereka mpata kuti bwaloli likonzedwenso malo ena monga posewerera mpira, dzimbudzi ndi mabafa, ngalande zake komanso m’malo okhalamo anthu zomwe zasemphana ndi maganizo a ku unduna wa zomangamanga omwe adapereka chilolezo kuti bwaloli ma timu a ku Blantyre atha kumagwiritsabe ntchito akudikira kulikonza.

Pa za Bwalo la Karonga FAM yanenetsa kuti bwaloli likuyenera kuyang’anilidwa pamene akulikonzabe kaye ndipo kuti litha kudzapangitsa masewera m’ma sewera a chaka cha mawa koma osati chaka chino.

Bungweli ladzudzulanso ma bwalo omwe alandira chilolezi kuti akuyenera kukonzabe mabwalo awo masewera asanayambe pa 6 May chaka chino.

Koma funso lomwe layimitsa mutu wa zizwa mkumati, kodi SULOM itani ndi m’ndandanda wa masewero omwe linayika kuti achitikire pa Kamuzu mu sabata yoyamba ya ligi?

Dzilolezodzi dzadza poyang’ana ndondomeko ya Football Association of Malawi (FAM) yopereka dziphaso kwa ma timu ija pa chizungu amati club licencing system.

Advertisement

One Comment

  1. Mutu ya Anthu akumalawi’fe penapakeee siikugwira bwinoo, dzinthu zoti mkanawaudza pakeleroo anthu mkuwaudza Lero while pa 6next Month ndiye mkuganidza kut akhodza liti zinthidzooo

    Thinking capacity is very low (FAM)

Comments are closed.