Aphedwa ndi njati ku Machinga

Advertisement

Bambo wina m’boma la Machinga wamwalira atavulazidwa mochititsa mantha ndi Njati yomwe inathawa ku malo osungira nyama za mtchire a Liwonde m’bomalo.

Malingana ndi oyankhulira apolisi ku Machinga Davie Sulumba, mkulu waphedwayu ndi a Steward Mapanga a zaka 44.

A Sulumba anati a Mapanga monga mwa nthawi zonse anapita kumunda wawo wa chinangwa m’mawa wa tsikuli kukalima.

A Sulumba anaonjezera ponena kuti pa tsiku la tsokali a Mapanga anamva mfuwu wa mayi yemwe amakolora m’munda mwake pafupi ndi munda wawo, kuwadziwitsa kuti abisale kukudutsa nyama yolusa kwambiri.

“Posatengera kuti awonetsetse kuti nchani chikudutsa a Mapanga anabisala ndipo Njatiyo inadutsa mothamanga,” anatero a Sulumba.

Powona kuti inali Njati, a Mapanga anaitsatira, koma Njati yomwe ndi nyama yomwe sidziwika kuti mu mphindi zotsatira ipanga chani komanso ndi yoopsa kwambiri kwa munthu itawaona inawatembenukira nkuyamba kuthamangitsa a Mapanga ndipo idawapha powabowola ndi nyanga pa mimba.

A Mapanga anamwalira atangofika kumene ku chipatala cha Chikwewo m’bomalo kamba kotaya magazi ambiri.

Anthu ozungulira anadziwitsa oyang’anira nkhalangoyi koma asanafike iwo kudzaikusa nyamayi anthu a m’mudzi anayisaka mkuipha ndipo anagawana nyamayo.

Mapanga anali ochokera m’mudzi mwa Matchina mfumu yayikulu Chikwewo m’boma lomweli la Machinga.

Advertisement