Akugulitsa chithandizo analandila chija

Lilongwe floods

A Malawi24 tatsimikiza kuti Anthu ena amene anakhuzidwa ndi kusefukila kwa madzi mu boma la Lilongwe, tsopano ayamba kugulitsa wina mwa katundu amene anapatsidwa ndi Anthu akufuna kwabwino.

Malinga ndi kafukufuku wathu, Anthu amene anapezedwa ndi vuto la kusefukila kwa madzi pano akupikisana kupinyolitsa katundu uja. Ati watentha kwambiri pa msika ndi ufa wa phala, wa Vital Meal.

“Ena akuuvayitsa pa K1000 pamene ena akuuvayitsa pa K1500,” munthu wina anaulula.

Maboma a Lilongwe ndi Salima ndi amene anavutidwa ndi kusefukila kwa madzi chaka chino.

Advertisement