Mafumu akufuna amayi aziloledwa kuchotsa mimba – atelo a Lukwa

Advertisement
Man impregnates his sister; says they are in love
Senior Chief Lukwa of Kasungu
Mfumu Lukwa akuti mafumu ali mbali yoti azimayi aiztaya pakati.

Anthu a mipingo ndi ena onse amene akudana ndi lamulo loti amayi aziloledwa kuchotsa pakati asayese Mafumu ali mbali yawo.

Malingana ndi Mfumu Yaikulu Lukwa ya a Chewa, Mafumu akugwilizana ndi lamulo loti amayi aziloledwa kuchotsa pakati.

A Lukwa amene ndi mlembi wamkulu wa bungwe la Mafumu ati iwo monga Mafumu ali okonzeka kuchita zionetselo ngati aphungu akane kukambilana za lamulo limeneli.

“Takonzeka kuvala mikanjo yathu ya ulemelero ndi kupita ku nyumba ya malamulo komweko kukawauza a phungu kuti nkhani imeneyi tikufuna ikambidwe,” anatelo a Lukwa.

Iwo anaonjezelapo kunena kuti Anthu amene akudana ndi lamulo lochotsa pakati sanakhale ndi nthawi yowelenga zimene lamulo limeneli likukamba.

“Nkhaniyi ena angoyankhula mwaphuma, sanawelenge za lamulo limeneli ndi komwe. Anthu otelewa asatisokoneze,” anaonjezelapo.

Lamulo lovomela amayi kuchotsa pakati linakolela moto pakatipa a mipingo atachita chionetselo chokana kuti pakhazikitsidwe lamuloli.