29 October 2016 Last updated at: 7:40 AM

A Mutharika agula galimoto ya mamiliyoni ambirimbiri pamene a Malawi akuvutika ndi njala ndi kugona mu m’dima

Panthawi imene a Malawi ali pa mavuto a njala komanso kugona mu mdima, mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika azigulila okha galimoto yatsopano imene ikukwana ndalama zankhaninkhani.

2016-lexus

2016-lexus yopezeka pa intaneti.

Malingana ndi ma lipoti amene talandila a Malawi24, a Mutharika azigulila galimoto la mtundu wa Lexus limene likukwana ndalama zoposela K70 miliyoni.

A Mutharika anakwela galimotoli dzulo pamene amakhazikitsa ziphaso za mzika za dziko lino. A Mutharika anakwelanso galimotoli pa msonkhano wa chitukuko umene anachititsa pa Mchinji boma.

Galimoto la a Mutharika lagulidwa pamene a Malawi ena anadandaula kuti mkuluyi akuononga chuma cha boma ati pokhalitsa mu dziko la Amereka.

A Mutharika anakhala mu dziko la Amereka kwa mwezi watunthu atapita ku msonkhano wa mayiko a padziko lonse. Msonkhanowu unali wa sabata ziwili zokha koma a Mutharika anakomedwako mpaka mwezi.

Galimoto la a Mutharika layamba kale kudzetsa mpungwepungwe pakati pa a Malawi amene aliona.

A Felix Unyolo amene amakonda kulankhulapo pa nkhani zochitika m’dziko muno ati kugula galimoto pa nthawi ino pamene a Malawi akuvutika ndi kolakwika.

“A Mutharika akufunika mayendedwe a bwino koma osati pano pamene zinthu sizikuyenda. Uku ndi kuzikonda. Akanadikila kaye zinthu zizayende kuti iwo azagule gaalimoto limenelo,” anatelo a Unyolo.

 813 Comments On "A Mutharika agula galimoto ya mamiliyoni ambirimbiri pamene a Malawi akuvutika ndi njala ndi kugona mu m’dima"