Nkhani ku Joni ndi ya Gaba

Advertisement
Gabadinho Mhango

… Chifukwa walabvulira mzake

 Wadyanso wani Gabadinho Mhango mu dziko la South Africa.

Ambiri akukamba za iye.

Koma m’malo momuyamikila kuti ali ndi luso logometsa mafuko pokankha chikopa, anthu akuti khalidwe la Gaba ndi lonunkha ndi lomvetsa manyazi.

Gabadinho Mhango
Gabadinho Mhango: Ambiri akukamba za iye.

Anthu ambiri mu dziko la South Africa ayankhulapo mokhumudwa pa khalidwe lomwe wachita Gaba lolabvulira mzake kunkhope masewelo a mpira atavuta.

Gaba akuti analabvulila kunkhope osewela wina wa ku South Africa pamene kalabu imene amasewela ya Bidvest Wits imakumana ndi ina ya Amazulu ya komweko.

Panachitika ka mkokemkoke pakati pa Gabadinho ndi osewela wa Amazulu otchedwa Micheal Morton.

Pokokana paja, ati Gaba anathila mzakeyo malobvu kunkhope poonetsa kunyansidwa naye.

Oimbila sanaone zimene anachita Gaba ndipo pamene Michael Morton anamutafulila Gaba, oyimbila anatulutsa kadi lofiila kumuthamangitsa mu masewelo Morton ngakhale iye anali olakwilidwa.

Khalidwe la Gaba lakhumudwitsa okonda mpira a mu dziko la South Africa ndipo ena apempha kuti Gaba amupatse chilango.

Mphunzitsi wa timu ya Bidvest Wits kumene amasewela Gaba wati ngakhale sanaone mnyamata wake akuchita khalidwe losakhala bwinolo, afufuza ndipo akapezeka olakwa aona naye chochita.

 

 

Advertisement

200 Comments

  1. Akanaphunzira bwino, akanadziwa kuti malovu sitimaponyera kwa nzathu. Koma poti ………, atitukwanitsa ngati a Malawi tonse timakonda kulavulirana

  2. Munthu ukachuka kwambiri umayesa wafikapo.
    Nthawi yama nong’ono non’go nthawi ya kunva za khalidwe la Gaba.
    Zikuti bwanji?

  3. 56.3 It was not real saliva it was merely the sweat that runs down across his mouth. But still view the incident with impartial. The disciplinary committee may permit the proceedings to be conducted using, or including the use of, electronic media such as video or audio conferencing facilities where these are readily available or can be obtained and where it would prevent delay, save cost, be convenient and be in the interests of justice.

  4. Nkhani ivuta kwambiri chifukwa analavulira mzungu akanakhala wakuda mzake bola. Ndiye Gaba ayembekezere chilango chachikulu pa nkhani imeneyi tivomeleze sanachite bwino akanaganiza za umphawi anasiya kumudzi kuno asanapange zimenezo Football is a short term career make hay whilst sunshine

  5. Mr Zinedine Zidane anamenya munthu in world cup 2006 , izi zimatha kuchitika malingana ndi kupsya kwambiri .so let’s check both sides and see coursitive even court limamva mbali zonse , muyambe kaye mwapeza zifukwa osamangoti gaba walavula .koma ngati
    ili jealous tiyeni nayo

    1. Ur ryt but team spirit ndiyofunika muMpira,,zimachitikadi zambir but @ de end maPlayer amagwirana zanja..kuxonyaza umodzi. If u talk about Zidane ndi mbiri yake yaMpira, samaener kukhar chonchija..bwenz Ali paPick hvy, koma chifukwa chavuto lomwe anapanga lija salandila ulemu wokwanila ngati mmene zimaener kukhalir. Anyway ndikhani zaMpir zongocheza izi. Gud dae

  6. Gaba ndi mbuzi yochititsa wayamba kulavulira mapuleya anzake ngati njoka . Akakuyimitsa mpira uzichita chiyani? Mapeto ake uzikalima ganyu kwanu yokumba chinangwa kukasungu.

  7. All who Is player try to learn to calm down coz football is not part of fight,no matter what!! but you end up shaking hands dat is football I know.But the problem is when things start going better in terms of money you start feeling yourself sugar,being like you’re much important than else!!! Plz try to change be as a human being.

  8. #michal nkandawire #palibe zakuti media zomwe midia yakamba its exactly what I saw with my 2 naked eyes in all two games yomwe Akhala akumu heda Gaba nyamatayu ndiwathu tiyeni timuthandize ine wokhudzika heavy ndimachita manyazi kwa azizanga ma S Africans

  9. Ine Gaba mwana wa kwathu ndimamukonda koma w
    mdikhoza kunena kut akudzinva mwanjira ina kut zinveke bwino mukaonera masera ake iyeyo ndiemwe amayambitsa kut anzakewo adzimu heda chonvetsa chisoni ntimanyazi nchoti akamuheda sakumabwenzeranso Achimwe a Gaba ngat mukundinva ife timakukondani koma zivuta kukuikolani kumbuyo musinthe

  10. kkkkk a Malawi kufulumila kuweluza 2 much khani ikufufuzidwa ziwani Utsi sufuka popanda moto poweluza timayang’ana mbalizose ziwili mwina it’s siolakwa plZ phuzilani kupanga handle khani not judgmental

  11. Munthu wina aliyense akawawidwa mtima amatha kupanga chomwe wanganiza, chifukwa anthu amapezeka kut aphana. but the end amazipanga regret analakwisa

    Apasa nyamata wathu kut azipanga zimenezi, chilipo chinapangisa. Ndiye tisamuchule iyeyo kut ndiolakwa, iyeyo ndi munthu akuyenera kulakwisa or kubwezera chomwe wachitilidwa choipa

  12. Omse omwe akumunyoza gaba kuti tionesese ndi anamarila awa yakula ndi msanje m’malawi sazatheka munthu oipisisa ziko lomse la pamsi

  13. vuto ndikukampopi fc anachokera kuja, akamamukira mtima yeriya kananji nde akumaona ngati matsotsi ndisize yake, pamsana pake gabayo mumuuze

  14. Kodi Zinedine Zidane kuti amusumbe Matelaz chinachitika ndi chani? Nanga basi ya noma kuti igendendwe chinachitika ndi chiyani? What about this issue of Gabba?

  15. The work of ignorance,He forget that he earn a living because of dat carrier;MAPLAYER TAMALOWANI MKALASI KUTI MUPHUNZIRE HOW TO DISCIPLINE YOURSELF;;;;::KATENGENI MBULI INA YACHIWIRI NDI IMENEYI !!!!! NOMA WOYEEEE

  16. Mwina zimene anamulankhula ndizopweteka kwambiri kuposa kulavulilidwako musamaiwaletu ku Joni kuno anthu obwerafe amatiyankhula mosakhala bwino ndetiyeni tidikire kuti nkhani itha bwanji,tisangoiwonera nkhaniyi pamwamba mkumalankhura zambiri sibwino

  17. Media media media. Joni yake iti. That’s was a mistake. Gaba is a well behave player with good record. So stop feeding people nonsense. Media can tore celebrate easily. Kankhani kang’ono media chinkhani

  18. Zochitika mu mpila ndi zambili,camera ikhoza kuonesa view zomwe zachitika koma sitikuziwa kuti munthu amamulavulilayo anati chani kwa bwanawa?kapena anapanga zotani kwa bwanawa.mu PSL momwemo omenya mpilaso wina anamuheda Gaba zadala dala mpakana munthuyo analandila chitupa chofila kuti asapitilize kusewela mpila.ndiye ine pano sindikuti Gaba anachita zabwino ayi komano pena kumakhala kuphatikiza ndi kutopa

    1. Ndiye ndizimenezo lamulo lamulunjika. Zipenekelani mwina sadamulankhule bwino pano zolavulira mzungu zachita kuoneka. Sitingasekelele zopusazo. Ndiye zimenezo kasumeni PSL ilibe Za Walter Nyamilandu

  19. Bad. Tempered. Destructive comments from you Malawians. Let’s wish him a fair punishment. Yes. Walakwa alandire Chilango koma ndi Mmalawi nzathu.

  20. Kkkkk wachingambwe ndi wachingambwe olo patadusa zaka 10 koma mmutumo mmakhalabe kut chingambwe chikugwila. ntchito musadabwe naye uyu vuto ndi komwe anachokela ku chingambwe FC. Kkkkkk

  21. Fokolo zanu mukungoti gaba gaba walakwa, walakwa chiyani kuzolowela kupusa pamaso pamzungu basi mbuzi nose
    Ndikutitu aliyese alipile mbuzi oky

  22. Palibepo chachilendo apa mukamakhala musamaiwale kut Gaba anachokera ku Bullets ndipo athu ose osatila bullets ndi osewera omwe alibe khalidwe kaya ndi ufiti kaya ndikudelera

  23. Vuto ma player mumakonda zolavulalavula mu ground ngati mwadya xowawa mwinaso gabayu samafuna kumulavulira koma mu nkhalidwe wolavula mu ground wamupachikisa

  24. Mmmm i see no reason of blaming him , nkhani yama emotions ndi individual difference . Even identical twins have different emotions

  25. Gaba over reacted komanso titati timve zomwe mzunguyo analankhula ndibwino coz munthu sungamulavulile atakuyankhula bwino…mzungu anatukwana

    1. Sakudziwa world cap inayake zidan anamuheda preyar mzake chifukwa cha kulankhula mau opusa. anthu ambili amalankhulila kaduka tiyeni tivomeleze kuti gaba zake zinayenda.

  26. Sitidziwa zomwe olavuriridwayo adanena kwa Gaba,pasanafike poti iye(Gaba,)alavule ,Bidvest yanena kuti ithana ndi nkhaniyi mwa iyo yokha ,ife tiyeni tizikazinga chimangachi apa

  27. AdaGABA UKUPITILIZA ZOMWE ZIDANE,SWALEZ kuluma,kuhedana linali lusolawo MDIYEIWEYOWANGOYAMBA PITILIZA UZATHE NGAT AZAKO LIMBIKILA ukunva!! Kkkkkk

  28. Munthu wina aliyense ali ndizofooka zake.Palibe yemwe ali 100% kalipo kalipo komwe kapangitsa kut atelo.Ndie anthu musathe mau.Sizachilendo zoipa zimachitika kupotsa apa.Bwanji munthu amapha munthu nzake?Bwanji nkazi wa Robert Mugabe anapanga nkhanza mtsikana wina ku SA komweko? anthu yakula ndinsanje kusamfunila zabwino.

  29. zalakwika polavulila nzakeyo… komaso a Malawi osamafulumila kumunena mwanayi kuti ndi mbuli cz simunaone zomwe zamupangisa iye kuti alavulile nzake, enanu mumaphya ntima ndikuchitaso react kuposa mene wapangila nkuluyi… nkhani ndiyoti angopasidwa chilango akapezeka olakwa kuti asinthe khalidwe.. koma osati mupezele mpata paumbuli wake, nzanu akudya money.

    1. Sizobisa ndimbuli kumene ife sitingasekelele nkhalidwe opusawo. Sitikukamba za kudya makwapala aliyense amazidyesa. Sangatengele chitsanzo Chabwino anthu monga: Maduka,Mabedi,Mwafulirwa,Kanyenda,Mgangira,Kamwendo,Mwakasungura,Mponda,Msowoya,Chimodzi,Sangala,N,’gambi,Anong’a,Chancy Gondwe, livewire Enerst Chirwali Mtawali.

    2. Anthu kutha mau kwambiri
      Sitikudziwa kuti Morton analankhula mau owawa bwanji.
      Pena anthu akuno Ku RSA salankhula bwino kwa obwera maka akakuwona kuti u r on top.
      I remember Zidane headbutted player wa Italy anthu adatha mau after atapita ku hearing panapezeka kuti Italy player anamtukwanila zidane makolo ake kuti They r Terrorist.
      So let’s wait and see the outcome after hearings.

    3. Umbuli wauyamba si Gaba kuno Ku RSA President ndi nbuli number one padziko lonse lapansi, so why Gaba?
      Akukamba zaumbuliwa nde number one Mbuli poti apa sitiikapo mapepala a Ku school

  30. School ndiyofunika kwambili chifukwa pepa imakuthandizila kupanga ziganizo moyenela. Tione momwe zithele crying for my be loved Gaba

  31. Nkulu ameneyu akumachitsa manyazi,chifukwa chomwe ndikudziwa football is a shot time career ndipo umayenera kuyendalimodzi ndi khalidwe,afunse Ronaldihno,Mess,Thierry Henry anyamata andalama koma odzichepesa.

    1. musanene kut amachititsa manyaz and you have randomly selected those players Suarez mwamisiya kut ndi khalidwe lake lija …….he only failed to control his temper bas

    2. Remember, playing professional football you have to be professional in your characters too! He’s an example to all the youngsters,tell me can you be happy to see your talented son behaving like Baloteri,Diego Costa?

    3. Mukanakhara kuti mukuzindikira zomwe mukulankhura ndikanakuuza,koma poti mwabwera ndinkwiyo ipsyani zenizeni! anthu osamfunira mzanu zabwino.

  32. Sanalakwitse ….. player wina uja after atamugwetsa Gaba ref anamupatsa yellow card ndiye uyu mzunguyi kuzolowera racism amamukankha Gaba nkumamutukwana … anamuchita bwino kumulavulira kumaso ndipo anachepetsa
    .. ma Buno kuzolowera nkhanza

    1. Anamukankhilanji … i watched the game simukudziwa zomwe zinachitika … ma Buno amatukwaba kwabasi and being a foreigner amanyozedwa

  33. Ine ndiwa Big Bullets weniweni koma zomwe Gaba adachita ndizochitsa manyazi a Malawi fe chifukwa kunoku ena ayamba kale kunena kuti zimenezi akapangire kwawo ku Malawi kudonyeza kuti salinso pamtendere. Xenophobia waiputa yekha Gaba. Ndiponso Gaba sakutha kudzigwira mtima panopa adafika pokula mtima kwambiri. Osatengerako chitsanzo chabwino cha Robert Ng’ambi kuti mpira umafunika discipline

  34. Sizachilendo tikatengera ma players ochoka ku bullets amakhala mbuli ndipo kutchulapo ochepa ndi Gaba komanso Sailesi amene sukulu inawavuta

    1. Nawenso ndikape!!!! zikugwilizana bwanji ndisukulu komanso #bullets ?Iweo ndisukulu yakoyo umapanganao chani choti anthu mkukuziwa nacho mbuzi iwe?

    2. U r too an idiot, how much r these boyz geting per month? Even educated people sometimes show such behavior. Sibwino kunyoza osaphunzira ngati kwanu kuyambira ambuyako mpaka nose ndinuophunzira ndiye kuti ndinu amwayi.

    3. #patrick komanso #shadrick mukungoonetsera mtima wakaduka. chabwino ife ndimbuli #abullets komano zathu zikutheka.Kumbali ya Gaba angakhale mumunyoze chotani simuzafika paiye ndisukulu yanuyo.Ngati muli ophunzila kwambiri mumapanga chani muli ndichani?

    4. Yes sanamalize school yake koma I can tell u kuti gaba speaks nice English yoti enanu simungathe am with him most of the time and he is a good guy

  35. Ana a neba sasowa kupanda khalidwe eni wakewo akutsangalala ati waika team ya bullets pa map kkkkkk masavege awa sadzatheka basi

  36. Alangidwe watha mantha kulavulila mzungu . #kuda_kwathupi_ndi_mtima_omwe. Wangokhala mmalawi mzanga apa Ndiye siudachite zampira. Kudali #Don_Pahuwa goalkeeper wa silver panthawiyo adapanga zolavulila muchakudya chamzake ku camp ya flames koma pano adangosowa ndi kuzima kuti ziiiiii sindikudziwa ngati alimoyo.

  37. Hello wonderful friends and my country people this is a testimony of how God cured me from HIV/aids through Dr Abuu, I never believed it I used to cry everyday thinking i will die someday,i have being suffering from hiv/aids for the past 7 years without the expectation of being cure, i was on ARV, despite the ARV i was not comfortable and there was nothing i could do because i knew and i was told by my doctor that there is no cure for HIV/AIDS, my dream of getting cured came to past the day i came across a testimony like this on a Facebook page of how someone was cured through the help of Dr Abuu herbal medicine,i was advice its not real that there is no cure but i summon the courage and i decide to contact him after some discussion with him on how the cure works and how to get it, the cure was sent to me and i used it according to how i was told to use it, during the first week i could noticed the change in my body after the completion of the medicine i went for a test which shows negative i could not hold back the tears of joy running down my face my doctor was shocked, i never believed there is a cure, then i decides to post it on social media so that anyone who is positive or has anyone who is positive can contact Dr Abuu and get cured, you can whatsapp him on +2348066454364 and his email address is [email protected], my happiness has no limit ever since my results has showed me negative.

    1. Mmmm! Apa palibe za school brother musaiwale kuti school imangochotsa umbuli chabe koma uchitsiru umakala ulipobe izoo mudziwe brother

    2. iwenso ndi mbudzi bwanji ,kumarawiko kuli anthu angati ophuzira ndipo ali ndi chani kuphatikiza iweyo ndi agogo ako,ukazalembanso mbwelera zimenezi suzarandiranso makopo kuphatikiza akwanu onse mbuziwe

Comments are closed.