Zina ukamva kukamwa yasa, anthu okhala m’mudzi mwa Phanisa m’boma la Mulanje usiku wathawu agenda ndi kuvulaza alendo okawona phiri powaganizira kuti amakayika zipangizo zomwe zibweretse namondwe wa Chido m’phiri la Mulanje.
M’neneli wa apolisi Ku Mulanje watsimikizira wailesi ina m’dziko muno ponena kuti anthu okwiyawa aphwanya Ambulance ya pa chipatala cha Mulanje mission pamene inapita limodzi ndi ngalimoto la apolisi kukapulumutsa anthu okhudzidwawa.
M’modzi mwa opelekeza alendo mphiri la Mulanje a Robert Korea ati anafotokozera anthu okwiyawa za ulendo wa anthuwa mphirimu koma anthuwa anasankha kusamva ndi kuyamba kugenda ndi kuvulaza ena mwa asanuwa.
Alendowa omwe ndi Sean Phata, Grace katondo , Christopher Chimenya ndi a Felix Tembo omwe amagwira ntchito pa chipatala cha Mulanje mission, Jimmy Kaphani yemwe ndi mphunzitsi pa sukulu ya St Philomena, Jones Matemvu omwe amagwira ntchito ku zakhalango komanso mtsikana m’modzi Mirriam Banda.
Malingana ndi a Jones Matemvu, anthuwa anagwetsanso mbali ina ya khoma lanyumba ya a mfumu a Phanisa omwe izi zimachitikira m’mudzi mwawo, iwo anayamika apolisi ndi achitetezo cha m’mudzi pobwera mu nthawi yake kudzawapulumutsa.
Pakadali pano apolisi sanagwire aliyense yemwe akukhudzidwa ndi mchitidwe owoopsawu.
A zanyengo akhala akupeleka ma uthenga kudzera pa lamya kuti anthu asamale pamene kukubwera namondwe otchedwa Chido kuchokera ku nyanja ya mchere ya Indian kudzera ku dziko la Mozambique ndipo ati namondweyu akhudza maboma ambiri a ku chigawo cha ku m’mwera.