Yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha United Democratic Front (UDF) ku chigawo cha ku m’mawa a Hashim Banda ati masomphenya a chipani cha United Transformation Movement (UTM) anawakopa ndi chifukwa alowa chipanichi.
Poyankhula pa msonkhano wa ndale omwe chipanichi chinapangitsa pa bwalo la Chinamwali ku Zomba a Banda ati nzosabisa kuti dziko likuyenera kudziwa kuti mfundo ndi masomphenya a chipani cha UTM ndi a mphamvu komanso ali ndi kuthekera kosintha zinthu, iwo ati zipani mdziko muno zimawafikira kuti azitumikire pamene anangotula pansi udindo ku UDF koma anasankha masomphenya a tsogolo ndi chifukwa alowa UTM.
A Banda omwe mu masankho a 2019 anapikisana nawo pa mpando wa phungu wa dela la pakati m’boma la Zomba ati akapikisana nawonso pa mpandowu pa masankho amene akubwera chaka cha mawa ndipo atsimikiza kuti akapambana.
Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM a Patricia Kaliati ati manifesito a chipanichi ndi kudzakwanilitsa zomwe analonjeza kale mu manifesto yawo, ndipo kubwera kwa adindo akulu-akulu ena ku chipanichi ndi umboni wa kuthekera ndi tsogolo lomwe chipanichi chili nako.
A Kaliati ati mavuto amene dziko lino likukumana nawo akuyenera kutha chipanichi motsogozedwa ndi mtsogoleri wawo a Saulos Chilima akadzalowa m’boma chaka cha mawa ndipo ati manifesito yomwe ikugwiritsidwa ntchito pakadali pano si a UTM.
Pa msonkhanowu anthu ena oposa makumi asanu alowa chipanichi kuchoka ku zipani za DPP ndi UDF.